Mchitidwe osiya kumwa mankhwala a khate ukuchulukira — atero azaumoyo

Advertisement
Balaka hospital dermatologist Alexander Memayako

Mchitidwe osiyira panjira kumwa mankhwala a matenda a khate m’boma la Balaka waoneka kuti ukuchulukira zomwe zikupangitsa kuti odwala nthendayi asamachire nsanga.

Izi zadziwika pamene mkulu owona matenda apakhungu komanso a khate pa chipatala cha Balaka Alexander Memayako wauza atolakhani lachitatu kuti anthu omwe anapezeka ndi nthendayi akangowona kuti ayamba kuchira amasiya kumwa mankhwala zomwe zimapangitsa kuti nthendayi ipitilire mwamphamvu komanso mpakana osadzachiranso.

Memamoyo wati ngakhale boma limapereka ndalama yoti anthu odwala nthendayi azigwiritsa ntchito pamayendedwe awo pamene akupita kuchipatala, ena amapezeka kuti pamene alandira ndalamayi amagwiritsira ntchito pakhomo zomwe zimapangitsa kuti alephere kupita kuchipatala malingana ndi masiku awo okalandirira mankhwala.

Iye waonjezera ponena kuti ngakhale zili choncho, ena odwala nthendayi akuonetsa chidwi pomabwera kuchipatala pafupipafupi komanso pokumwa mankhwala mwandondomeko yoyenera.

“Pakadali pano matenda akhate akupitira kupezeka ndipo anthu akumachokera madera akutali monga ngati Ntcheu, Machinga , Dedza komanso komwekuno ku Balaka chifukwa boma lino kuli malo ake amene amapezeka anthu odwala matenda akhate,” anatero pofotokoza.

Memayako ananena kuti panopa akumayesesa kuti odwala khate alandire mankhwala ndipo amwe motsatira ndondomeko yoyenera yomwe amapatsidwa kuchipatala kutinso pasakhale mwayi opatsira matenda kwa anthu ena chifukwa munthu akamwa mankhwala amenewa kwa masiku atatu tidzilombo timakhala tikufa.

Adawonjezera ponena kuti akuyesesa kuti anthu adziwe za matenda a khate kuti akawona zizindikiro azipita kuchipatala mwansanga kuti akalandire chithandizo.

Utale, Mbera, Ulongwe, Mphimbi ndi madera omwe amapezeka anthu odwala khate m’bomali.

Anthu odwala matenda a khate m’boma la Balaka alipo 38. Mu mwezi wa Januwale kupita Epulo anapezeka anthu awiri, mu malichi mpaka Epulo anapezeka 10, Juni kupita sepetemba apezeka 12.

Advertisement