“Zeze ndili naye pulani” – Jetu achenjeza Cash Madam

Advertisement
Dorothy Shonga with her boyfriend Zeze. The two are set to get married in 2024

Eeyo! Tiyeni! Tiyeni! Tiyeni: ngakhale kuti “K100 miliyoni sindalama”, koma Dorothy Shonga akuyenera kuchengetera bwenzi lake Zeze Kingston ngati dzira kamba koti Jetu waopseza kutsomphora chikhwayacho. Ndi mkazi uti samafuna mamuna otulutsa K500, 000 yandiwo pa sabata?

Gogo Jetu abwera ndi mkokomo komaso moto omwe ukulilima kowopsa ndipo ngakhale kampani yozimitsa motoyo ikupeleweledwa nthanana kuti iwuzimitse, uwuwu ndi moto weniweni, siwamapesi ayi.

Chuluke chuluke ndi wa njuchi, umanena iyo yakulasa; Jetu ndioyimba watsopano yemwe wabwera patawuni pano ndipo ali ngati tsache latsopano lomwe limachotsa nyasi zonse mosavuta kamba koti nyimbo zawo zikuchotsa akangaude onse ankhawa m’miti ya anthu ambiri makamaka m’masamba a nchezo.

Jetu yemwe akuoneka wa mvula za kale, watulutsa nyimbo zingapo zomwe ngakhale kuti ndi zazifupi, zikuzura mitima ya anthu ndipo yomwe yatekesa kwambiri ndi yomwe wa chenjeza Dorothy Shonga kuti asamalitse mamuna wake Zeze ponena kuti ali naye pulani.

Nyimboyi yomwe ndiya msangulutso chabe, Jetu waulura kuti mamuna wa kale wa Tamia Ja Duncan Nyoni yemwe amasewera mpira mu timu ya Silver Strikers, ali ndi iye ndipo wachiwiri yemwe wagwa naye mchikondi ndi Zeze Kingston wa Cash Madam.

“Iwe ndi ndani? Ine ndi Jetu/Mamuna uja ndi wanga panopa ndamtenga ali ku nyumba kwanga/Lelo ali ndi ine Duncan Nyoni x2/Tamia Ja, wamuluza x2/lero ali ndi ine Duncan Nyoni.

“Watsala naweso Dorothy Shonga, Zeze ndili naye pulani, Ine ndi Jetu, Iyi lavu yu Zeze (I love you Zeze),” watelo Jetu munyimbo yatsopanoyo.

Pakadali pano, anthu ambiri m’masamba a nchezo akunyadira myimbo zomwe gogo Jetu akuimba.

Advertisement