Azungu abwereso adzagawane dziko la Malawi – watelo Kalindo

Advertisement
Bon Kalindo, Malawi's outspoken activist and opposition politician

…wati adzabwelera ku UTM ikadzatuluka mu Tonse

…wati Chakwera anawina chifukwa cha Chilima

M’modzi mwa anthu andale komanso omenyera ufulu, a Bon Kalindo, ati m’mene zafikira ndale m’dziko la Malawi pano mpongofunika azungu kuti aliyese adzipanga zake.

A Kalindo omwe anamangidwa posachedwapa ayankhula izi mupologalamu yapadera yomwe inakonza ndi wailesi ya Zodiak loweruka madzulo pa 2 September, 2023.

Mu pologalamuyi, mkuluyu yemwe amadziwikaso ndi dzina loti Winiko, wati zinthu m’dziko muno zafika pa mwana wakana phala kamba koti anthu ambiri mdziko muno amayamba ndale pongofuna kudzilemeletsa okha osati kufuna kuthandiza anthu am’madera omwe amayimilira.

A Kalindo ati pa chifukwa chimenecho iwo sakuona kufunika choti iwo akhazikike mu ndale ndipo ati nkwabwino kuti azungu abwereso m’dziko muno adzaligawane dzikoli kuti aliyese azipanga zomusangalatsa.

“Sindikuonapo chifukwa chokaimilira u MP kuti ndikakhale wa ndale pamene a Malawi akupitilirabe kumavutika. Nde kuli bwino dzikoli abwereso mwina azungu adzangoligawanapo aliyese azipanga zake.

“Zikanakhala kuti dziko limakhoza kugulitsidwa, dziko lina mwa dziko limene likanagulitsidwa linayenera kukhala dziko la Malawi kuti aliyese azipanga zake m’mene amapangira ana makolo awo akamwalira,” watelo Kalindo.

Iye anaululaso kuti ndi m’modzi mwa anthu omwe anayambitsa chipani cha UTM koma wati anatuluka chifukwa choti mtsogoleri wa chipanicho a Saulos Chilima anasankha kukhala mu mgwirizano wa Tonse yomwe a kuti ndiyolephera.

A Kalindo ati pakadali pano samayankhulana ndi a Chilima koma atsindika kuti iwo athaso kubwelera mu chipani cha UTM ngati chipanichi chitatuluka mumgwirizano wa Tonse.

“Ndimazimenya ndekha pansanapa kuti ndinayambitsa nawo chipani cha UTM ndipo silogani (Slogan) ija yoti ‘UTM Tsogolo Lathu’ ndinayambitsa ndi ineyo ku Ntcheu. Ndidzafa osangala chifukwa tinampanga Chilima m’mene alili muja ndi timu ya anthu ena koma mnaona kuti sakundipatsa ulemu chifukwa zimene tinawalonjeza anthu sizimene tikuzichita nde ine sindimakhala mbali ya anthu opanga zinthu zosokonekera.

“Ndipo Chilima atatuluka mu Tonse lero, ineyo mawa nditha kubwelera mu UTM. Panopa sitiyankhulana ndi Chilima koma munthu afune olo asafune, kaya amuda kapena ayi koma Chilima uja ndi amene anapangitsa kuti a Lazarus Chakwera awine chisankho chija.

“Chilima uja anakhala ngati watenga nyali yomwe anthu amaona kuwala mwa. Lero Chilima uja ndi mbali imodzi ya sisitimu (system) yoyipayo. Ndakhala ndikumawauza kumamiting’i ndili ku UTM kuti nthawi yotuluka mu Tonse ndiino,” anateloso Kalindo.

Iwo awuzaso dziko kuti anamangidwa mkati mwa sabatayi pa zifukwa zandale osati zomwe apolisi amanena zoti amalephera kukwanilitsa malamulo ena a belo (bail) yomwe anapatsidwa atamangidwa pa mlandu oti analumikiza magetsi mwachinyengo.

Apa mkuluyu anati akuganiza kuti anamangidwa pofuna kuti ziwonetsero zomwe amayenera kutsogolera zilepheleke ndipo wati mukumangidwa kwa awona zinthu zodabwitsa zosiyanasiyana zomwe apolisi amachita.

Advertisement