Apolisi alanda zigubu ku Lilongwe

Advertisement
Fuel jerrycans

Apolisi lero alanda zigubu zoposa 100 komanso mabotolo omwe anthu amafuna kuguliramo mafuta a galimoto ku Lilongwe.

Mneneri wa polisi ya Lilongwe a Hastings Chigalu ati apolisi alanda zigubuzi atayendera malo othirira mafuta a galimoto.

A Chigalu ati a polisi akufuna kuthana ndi mchitidwe wogula mafutawa ndi kumakagulitsa pa mtengo wokwera.

Lachiwiri sabata lino bungwe la Malawi Energy Regulatory Authority (MERA) linachenjeza kuti anthu onyamula zigubu asaloledwe kugula mafuta pamalo omwetsera mafuta.

Mu chikalata chomwe inatulutsa, MERA inati anthu ena akumagula mafuta ambili mu zigubu ndi cholinga chokuti akagulitsenso mafutawo pa mtengo okwera zomwe zikupangitsa kuti mafuta azipitilira kusowa.

Malingana ndi bungweli, kugulitsa mafuta mu chigubu opanda chilolezo cha MERA ndi kosaloledwa.

Bungweli linachenjezanso oyendetsa malo omwetsera mafuta m’dziko muno kuti asagulitse mafuta mokwera mtengo potengera mwayi kusowa kwa mafutawa.

Mtengo wovomerezeka wa petulo ndi K1,746 pa lita, wa dizilo ndi K1,920 pa lita koma ena akumagulitsa K5000 pa lita.

MERA inati malo omwetsera mafuta omwe apezeke akugulitsa pa mtengo wokwera kapena kugulitsa mafuta kwa onyamula zigubu azalandidwa zilolezo zochitira malonda ogulitsa mafuta.

Advertisement