BCC igumula nyumba zomangidwa malo osayenera

Advertisement
Floods Malaw

Khonsolo ya mzinda wa Blantyre yaopseza kuti igumula nyumba zonse zomwe zikumangidwa m’malo omwe ali pa chiopsezo chokhudzidwa ndi ngozi za chilengedwe monga m’mapili.

Izi ndi malingana ndi chikalata chomwe khonsoloyi yatulutsa lachiwiri sabata ino pa 1 August chomwe watikitira ndi mkulu wa khonsoloyi a Dennis Stan Chinseu.

BCC yati kumanga m’malo amene ali pachiopsezo chokhudzidwa ndi ngozi zogwa kaamba ka chilengedwe monga m’mapili komanso m’mphepete mwa mitsinje, ndikosaloredwa ndi malamulo oyendetsera khonsoloyi.

Khonsoloyi yati aliyese amene akumanga nyumba zawo m’madera oletsedwawa adzazengedwa mlandu, kulipitsidwa chindapusa komaso ati adzagumula nyumba zawo zonse mopanda chisoni.

“Khonsolo ya mzinda wa Blantyre ikudziwitsa anthu onse amene akukhala kapena akulingalira kukhala m’malo amene ali pachiopsezo cha ngozi zokudza chifukwa chachilengedwe (m’mapiri komanso m’mbali mwa mitsinje) kuti kumanga m’malo amenewa ndikoletsedwa.

“Khonsoloyi izazenga mlandu wina aliyense amene apezeke akumanga m’malo amenewa monyozera chidziwitso chimenechi. Khonsoloyi izagumula nyumba zonse zomwe zikumangidwa m’malo amenewa ndipo ndalama zonse zomwe zizagwiritsidwe ntchito pogumula nyumbazi zizatoleredwa kuchokera kwa amene azamange monyozera malamulo,” yatelo BCC.

BCC yati ena mwa malo oletsedwawa ndi ku mapiri monga Soche, Ndirande, Bangwe, Mthawira, Mpingwe, Nyambadwe komanso m’mbali mwa mitsinje yonse yomwe ikupezeka mu nzinda wa Blantyre.

Izi zikudza kutsatira ngozi ya madzi osefukira yomwe inadza kaamba ka namondwe wa Ana chaka chino, ngozi yomwe inapha anthu mazana mazana ndipo anthu omwe anakhudzidwa kwambiri ndiomwe amakhala m’mapili komaso m’mbali mwa mitsinje.

Advertisement