Anthu abwera atakhumudwa ku msonkhano wa NGC – watelo Dausi

Advertisement
Malawi Politician Nicholas Dausi

…wati ziphona zinkafuna kubilibinya Ken Nsonda ku msonkhanoko

…wati DPP ikufuna kubweretsa ma khadi kwa mamembala

Madzi akupitilira kuchita katondo ku chipani cha DPP pomwe zadziwika kuti ku msonkhano wa National Governing Council omwe unalipo posachedwapa, ambiri achokako atakhumudwa ndipo akuti a Ken Nsonda ankafuna kupatsidwa mabwande ndi ziphona.

Izi ndi malingana ndi ofalitsa nkhani ku chipani cha DPP a Nicholas Dausi omwe amayankhula zambiri zomwe zinamanga nthenje ku msonkhano wa NGC pomwe amacheza ndi wailesi ya Times loweruka madzulo pa 8 July, 2023.

Iwo anati ngakhale iwo sanapite ku msonkhano wa NGC wo kaamba koti anali ku khothi, amva kuti zambiri sizinayende ndipo ati ndi chifukwa chake akuwulura kuti pakhale kusintha kwa zinthu zina zomwe sizikuyenda bwino mchipani cha DPP.

A Dausi adandaula kuti malamulo atsopano a chipani cha DPP omwe akufuna kukhazikitsidwa, sakukomera mamembala enieni achipanichi ndipo a ena kuti ngati malamulowa angavomelezedwe, chipanichi chitha ngati makatani.

Apa anapeleka chitsanzo cha lamulo lomwe akuti lili pa mndandanda wa malamulo atsopanowa lomwe limkuti kuyambira mwezi wa December chaka chino, membala wina aliyese wa chipani azidula khadi zomwe akuti nzodandaulitsa kwambiri.

“Zambiri zomwe zinachitika ku msonkhanoko n’zotsamwitsa, n’zokhumudwitsa. Chavuta mchakuti ku NGC ko, ku msonkhano wa chipaniwo, anthu abwera atadandaula, amene anasankhidwa ngati mamembala a NGC mu 2018 abwera akudandaula chifukwa atapita kumeneko ajenda (agenda) ya kumeneko siinavomelezeke, sanaichite adopt.

“China akuti kuyambira December, ma membala onse a DPP azidula khadi la umembala wa chipani, akapanda kutelo umembala wa chipani uzikhala watha. Nde ine ndi kuti aaa tiyambeso kudula khadi? Ma khadi ake omwe aja anaononga Congress aja? Ngati Kamuzu ndi Malawi Congress anaipa dzina nkhani yake inali ya ma khadi. Zimenezi anthu amayenera apatsidwe mpata akambirane kaye zisanafike ku NGC,” anatelo Dausi.

Iwo adandaulaso ndi malamulo atsopano a chipani cha DPP omwe akuti akupeleka mphamvu kwa mtsogoleri wa dziko kusankha mlembi wa mkulu wa chipani osati kusankhidwa pa msonkhano waukulu ngati momwe zimayendera pano.

Dausi wadandaulaso za lamulo lomwe akuti lidzayamba kugwira ntchito DPP ikabwelera m’boma loti aliyese amene angadzasankhidwe kukhala kazembe wa dziko lino komaso udindo wa CEO ku makampani osiyanasiyana, akuyenera kumazapeleka K10 pa K100 iliyose (10 percent) ya malipilo ake.

Iwo ati ndalamayi idzidzapelekedwa ku chipani cha DPP ngati njira imodzi yothokozera kaamba kosankhidwa zomwe afotokoza kuti akuona kuti sizoyenera.

“Nde akuti kwakozedwa kuti kuyambira December chaka chino pulezidenti ndi amene adzisankha mlembi wankulu wa chipani yemwe akuyenera kukhala ndi Masters Degree, zomwe sizinachitikepo. Nde ndikuti bwanji osasiya kuti mlembi wankulu azisankhidwa ndi anthu ku koveshoni bwanji?

“Chinaso akuti DPP ikadzabwelera m’boma munthu aliyese amene azasankhidwe kukhala ambasada komaso maudindo a CEO ku makampani monga; ESCOM, ADMARC, Gaming Board, ma Water Board ndi ena ambiri, adzipeleka 10 pelesenti ku chipani cha DPP. Izi akuti zili mu malamulo atsopanowo,” anaonjezera Dausi.

Iwo anapitilira ndikudandaulaso za lamulo la tsopano loti mtsogoleri akaluza mpando ku koveshoni, adzikhala patiloni wa chipani komaso azikhala membala wa komiti yaikulu komaso azisankha aphungu khumi (10) kukhala mamembala ku NGC osati zomwe zimachitika pano zoti phungu aliyese amakhala membala wa NGC.

A Dausi omwe ndi phungu wa nyumba ya malamulo m’boma la Mwanza ati chodandaulitsa kwambiri mchakuti anthu kumkumanowu sanapatsidwe mwayi oti ayankhule zomwe ati ndizolakwika ponena kuti chipani kuti chikhale ndi mphavu, chimayenera chizivera maganizo a anthu ake.

Mkuluyu wati ziphona zina zomwe zinali ku msonkhanowo zinkafuna kumenya anthu amene amawonetsa kufuna kubweretsa maganizo osiyana ku nsonkhanowo kuphatikizapo a Nsonda.

“Kunalibe mwayi oti anthu ayankhule, umufuse Nsonda, Botomani, Chilenga, anaima koma sanapatsidwe mpata kuti ayankhule, mwayi umenewo kunalibe, Nsonda anaima maulendo asanu (5) mpaka ankafuna kumumenya makofi. Kunaima anyamata adzitho kumuuza kuti akhale pansi, nde chimenecho nchiyani? Ufulu? Demokalase?” wadabwa Dausi.

A Dausi ati a krona kuti ena mwa mavuto omwe ali ku chipanichi akubwera kaamba koti chipanichi sichinakhalepo pansi nkukambirana za tsogolo la chipani chawo chiluzileni zisankho za 2020.

Iwo alangizaso atsogoleri a chipanichi kuti malamulo omwe akufuna kusinthidwawo awapeleke kwa mamembala a NGC kuti nawo akafuse anthu akumadera kwawo ngati zina zomwe zikufuna kusinthidwazo zili zolondora.

“Ndiwapemphe kuti malamulo amene akufuna kusinthidwawo apelekedwe kwa membala aliyese wa NGC kuti nawo akafuse kwa anthu mmadera awo. Nzovetsa chisoni kuti palibe ndi mmodzi yemwe amene wapatsidwa chikalata cha malamulo omwe akufuna kusinthidwawa,” anafotokozaso Dausi.

Iwo ati anakakonda kuti chipani cha DPP chisasinthe malamulo ake pano koma ati malamulowa adzasinthidwe ikachitika koveshoni.

Advertisement