Wagwa mtengo ku St. Andrew’s Primary; pano fizi ndi K2.8 miliyoni yokha basi

Advertisement

…yolembetsera yokha ndi K372,750

Maphunziro ndi chuma kapena chuma ndi maphunziro abwino? Nzothekadi kuchepetsa mlingo wakusiyana pakati pa olemera ndi osawuka? Pomwe inu mukukanika kulipira K5000 kuti mwana wanu adziwe kunena kalenda-kalenda, afabeti ndi mavawelo, pano kalasi yotchipitsitsa ku St. Andrew’s International Primary School (SAIPS) ndi K750,000, akuti angokhwefula basi.

Izi ndi malingana ndi uthenga omwe tsamba lino lawona omwe sukuluyi ikutambasula bwino za mitengo yake yatsopano m’chaka cha maphunziro cha 2023/2024 yomwe akuti ndi yotchipa kuyelekeza ndi mitengo ya mbuyomu.

Mitengo ya tsopanoyi ikusonyeza kuti kalasi za ana ang’onoang’ono, osakwana chaka (toddler and pre-nursery), fizi yake yafika pa K750,000 kuchoka pa K950,000 koma kwa ana omwe amalipililidwa fizi ndi komwe makolo awo amagwira ntchito, fizi ili pa K902,500.

Kuchoka apo ana akalasi ya nkomba phala, fizi yawo yatsitsidwa kuchoka pa K950,000 kufika pa K850,000, pamene kuyambira kalasi ya lisepishoni mpaka kalasi ya chaka cha chisanu ndi chimodzi (reception to year 6), fizi yawo yakhwefulidwa kuchoka pa K3,150,000 kufika pa K2,835,000.

Kwa ana omwe amalipililidwa fizi ndi komwe makolo awo amagwira ntchito, fizi m’makalasi a lisepishoni mpaka chaka cha chisanu ndi chimodzi, fizi yawo ili pa K3,150,000 ndipo ana ochoka mayiko akunja m’makalasi omwewa akupeleka K3,561,000 kuchoka pa K5.4 miliyoni.

Kupatula mitengo ya fiziyi, ophunzira aliyese amayenera kupelekaso ndalama yokwana K372,750 akamalembetsedwa ndipo kwa ana omwe akanidwa ndi sukuluyi pa zifukwa zina, ndalamayi siyimabwezedwa.

Kuwonjezera apo mwana aliyese pa sukuluyi yomwe ili mumzinda wa Blantyre, amayenera kupeleka ndalama ya chitukuko yokwana K152,250 komaso K152,250 ya mabuku yomwe imadzabwezedwa ngati ophunzira wabweza mabuku onse akamachoka pa sukulupa.

Izi zikutanthauza kuti mwana m’modzi yekha kuti aphunzire maphunziro aku pulaimale (primary) pa sukuluyi, akuyenera kukhala ndi ndalama yosachepera K4 miliyoni.

Mitengo ya fiziyi mumasukulu ngati awa yakhala ikubweletsa mtsutso wosatha ngati ndizothekadi dziko lino kuchepetsa kukula kwa mlingo omwe ulipo wa kusiyana kwa pakati pa anthu olemera ndi osauka.

SAIPS ndi imodzi mwa sukulu zomwe mitengo ya fizi ndiyokwera kwambiri ndipo ophunzira ambiri pa sukuluyi ndi ana amabwana okhaokha ndipo ena amalipililidwa fizi kuchokera ku ma kampani komwe makolo awo amagwira ntchito ndipo enaso ndi akunja.

Kutsitsidwa kwa mtengoku kukudza pomwe posachedwapa panali mpungwepungwe wa umwini wa sukuluyi yomwe boma kudzera kwa oliyimilira pa milandu a Thabo Chakaka Nyirenda anati ndi ya boma.

Chakaka adalankhula izi ku bwalo la milandu la High Court mumzinda wa Blantyre mu December chaka chatha pa mlandu omwe makolo 83 a ophunzira pasukulupa anatenga chiletso choletsa mathilasiti (trustees) kugwira ntchito yawo.

Oyimilira boma pa milanduyu adalowa nawo pamlanduwu ndipo akufuna kuti sukuluyi ikhale pansi pa unduna wa zamaphunziro monga momwe zidalili mu nthawi ya mtsogoleri oyamba wa dziko lino, Hastings Kamuzu Banda.

“Sukuluyi ndi ya boma chifukwa palibe umboni owonetsa kuti inapelekedwa kwa ma thilasiti (trustees). Choncho ikuyenera ibwerere mmanja mwa boma. Fizi pa sukuluyi ndiyopitilira K3 miliyoni, kodi izi mzopindulira anthu onse m’dziko muno?” Anadabwa Chakaka Nyirenda.

Advertisement