Thilaki yagwetsa nyumba yapolisi ku LIlongwe

Advertisement

Galimoto lina la mtundu wa thilaki lagwetsa imodzi mwa nyumba za apolisi pa C-Company pafupi ndi Simama Hotel ku Lilongwe pomwe linasempha msewu

Galimotoyi lomwe lili ndi number plate ya m’dziko la Zambia ndipo inanyamula matumba a simenti imachochokera mbali ya ku Lilongwe girls secondary school.

Malingana ndi mneneri wa a polisi pa chigawo chapakati, Alfred Chimthere wati ngoziyi yachitika chamma 2 koloko mamawa wa lero.

A Chimthere ati zikuonetsa kuti dalaivala wa galimotoli anamwa mowa ndipo atafika pa Simama Hotel adaikhotetsera galimotoyi ku manja kwake komwe linakathera mu imodzi mwa nyumba zokhala a polisi zomwe zili mphepete mwa nsewu.

Iwo anaonjezera kunena kuti mwachisomo mnyumbayi munalibe aliyense pa nthawiyo ndipo palibe wavulala.

Padakali pano dalaivala wa galimotoyi ali mmanja mwa apolisi.

Advertisement