Anandiyimitsa udindo popanda chifukwa: yadandula mfumu yaikulu Amidu ku Balaka

Advertisement

Mfumu yaikulu Amidu ya m’boma la Balaka yadandaula kuti akuluakulu a khonsolo ya Balaka adaiyimitsa pa udindo wa ufumu pa zifukwa zomwe sakuzidziwa.

Poyankhula ndi Malawi24, mfumuyi, yomwe dzina lake lakubadwa ndi Amina Gayesi, yati kwa miyezi isanu ndi iwiri tsopano, iyo yakhala isakulabadilidwa mu misonkhano komanso zochitika zosiyanasiyana zokhudzana ndi khonsoloyi.

”Ndidalandira uthenga wakuti andiyimitsa pa udindo wanga ngakhale kuti sadandifotokozere zifukwa zake ndipo ine ndinali odabwa kwambiri,” mfumuyi idafotokoza motero.

Poyankhulapo pa dandauloli, bwanamkubwa wa boma la Balaka a Darwin Mngoli adatsimikiza kuti mfumuyi idaimitsidwa pa zifukwa zina.

”Ndi zoona kuti tidawaimitsa a mfumu Amidu pa udindo wawo chifukwa pali nkhani zomwe tikufuna tifufuze. Padakalipano takonza kuti tiwayitanitse a mfumuwa ku zokambirana zomwe zikuyembekezeka kuchitika sabata ya mawa,” adafotokoza motero a Mngoli.

Mfumu yaikulu Amidu idavekedwa kukhala mfumu yaikulu mu June chaka chatha.

Follow us on Twitter:

Advertisement