Khansala Rams Kajosolo wa Mtiya Ward mu Mzinda wa Zomba wamwalira

Advertisement

Khansala wamdera la Mtiya Ward mu Khonsolo ya Mzinda wa Zomba yemwe adali wachipani cha People’s Party (PP) Rams Kajosolo wamwalira pachipatala chachikulu cha Zomba m’bandakucha wa tsiku lachitatu atadwala matenda akuthamanga kwa magazi.

Wofalitsa nkhani za Khonsolo ya Mzinda wa Zomba Sylvia Thawani watsimikiza zankhaniyi ndipo wauza Malawi24 kuti Khansala Kajosolo wamwalira atadwala nthawi yochepa chifukwa chavuto lakuthamanga kwa magazi.

Thawani wati maliro ayikidwa mawa Lachisanu kumudzi kwao ku Mdeka Boma la Blantyre ndipo akuyembekezeka kunyamula thupi lamalemu Khansala Kajosolo kunyumba yachisoni yachipatala chachikulu cha Zomba masanawa kupita nawo kumudzi kwao ku Mdeka.

Malemu Khansala Rams Kajosolo adawasankha pachisankho cha 2019 ndipo akhala paudindowo kwa zaka zinai.

Mzimu wamalemu Khansala Rams Kajosolo uwutse mumtedere.

Follow us on Twitter:

Advertisement