Thilaki yapsa pa msika wa Mpondabwino ku Zomba

Advertisement

Galimoto ya mtundu wa thilaki yapsa yonse madzulo a lero Loweruka kwa Mpondabwino mu mzinda wa Zomba.

Galimoto yothimitsa moto yochokera ku Khonsolo ya mzinda wa Zomba idalephera kuthimitsa motowo ndipo madzi adawathera akuthimitsa motowo.

Chomwe chayambitsa motowo sichikudziwika komanso eni ake agalimotowo pakali pano sadadziwike.

Pakalipano palibe munthu yemwe wamvulala pangoziyo.

Follow us on Twitter:

Advertisement