Boma lisamutsa msasa wa Dzaleka kuchoka ku Dowa kupita ku Chitipa

Advertisement

Boma lati lili ndi ganizo losamutsa msasa wa anthu othawa kwawo kuchoka ku Dowa kuti ukakhale m’boma la Chitipa.

Izi lichita pofuna kuchepetsa kudzadzana kwa nzika za maiko enazi ku msasaku komanso pofuna kutsatira malamulo a dziko lonse lapansi oti msasa uzikhala makilomita 50 kuchokera pa chipata chadziko ndi dziko lina.

Nthambi yowona umoyo wa anthu othawa kwawo yanena izi dzulo pomwe komiti yoona zamaubale a dziko lino ndi maiko ena inayendera msasa wa Dzaleka ku Dowa pofuna kukaona m’mene nzika zamaiko ena zikukhalira.

Mkulu wa nthambi yowona umoyo wa anthu othawa kwawo commissioner General Ignacio Maulana anati nthambiyi imayang’ana malo m’maboma a Karonga, Mzimba ndipo pamapeto pake yapanga chiganizo chosamutsira msasawu m’boma la Chitipa pofuna kuchepetsa kudzadzana kwa anthu ku msasa wa Dzaleka.

“Padakali pano chatsala nkukaona malowa ndikupereka malipoti kwa adindo ndipo malowa ndipafupifupi ma hekitala 1000,” anatero a Maulana.

Iwo anaonjezera kunena kuti nthambiyi inalandira ndalama pafupifupi K800million kuchokera ku boma.

M’mawu ake, wapampando wa komiti yowona za maubale a dziko lino ndi maiko ena Patrick Siyabonga Bandawe anati komitiyi itayendera msasawu yawona kuti nzika za maiko ena zikukhala movutika chifukwa chakudzadzana.

Komabe iwo ati komitiyi ikuyamikira maganizo a nthambiyi opeza malo ena, komabe iwo anapempha boma kuti liwalole anthu omwe anasiya katundu wawo m’madera adziko lino kuti akatenge.

“Pakuti ifeyo ndife anthu komanso iwowanso ndi anthu, timaona kuti munthu anali ndi katundu wake ndipo amupeza mwadzidzi ngakhale kuti boma linatengabe nthawi kuwalangiza koma m’madziwa kuti anthu ena amakhalabe nkhutukumve, timaona ngati kuti pakhale njira yabwino kuti boma kudzera kwa anzathu a polisi athandizire kuti anthu amenewa akatenge katundu wawo nkubwerelanso ku msasa,” anatero a Bandawe.

Pofika dzulo, nzika za maiko ena 1,712 ndizomwe zabwelera ku msasa wa Dzaleka chiyambileni boma kusamutsa anthuwa kupita ku malowa, nzika zonse ku m’sasaku zilipo 50,615.

Ambiri mwa anthuwa ndi ochoka m’dziko la DRC ndipo alipo pafupifupi 32,000.

Follow us on Twitter:

Advertisement