Mzimayi ogulitsa thupi wabaya kasitomala malo obisika

Advertisement

Apolisi ku Monkey Bay m’boma la Mangochi akusunga mchitokosi mzimayi oyendayenda kaamba kobaya kasitomala wake malo obisika pa nkhani ya malipilo.

Malingana ndi ofalitsa nkhani pa polisiyi ya Monkey Bay Sergeant Alice Sichali, mzimayi ogulitsa thupiyu wazindikilidwa ngati a Patricia Wyson yemwe anapalamula mlanduwu usiku wa lachisanu pa 28 April.

A Sichali ati nkhaniyi yachitika mmudzi wa Chembe ku Cape Maclear m’dera la mfumu yaikulu Nankumba m’boma la Mangochi.

Iwo ati lachisanu usiku, oganizilidwawa omwe ndi a zaka 29 anakumana ndi mzibamboyu malo ena m’mudzimo ndipo kenaka anatengana kupita kunyumba mzimayi ogulitsa thupiyo.

Kutenganaku kunali kaamba koti awiriwa chilengedwe chinali chikuwavutitsa ndipo anagwirizana kuti akagonane ku nyumba ya mzimayi ogulitsa thupiyo pa mtengo wa K1,000 kwacha.

Atamaliza macheza awo, awiriwa anasemphana chichewa pankhani yomwe ikuoneka kuti ndiyokhudza K1000 yamalipilo yomwe anagwilizana, ndipo mayiyu anatenga mpeni ndikubaya bamboyu malo obisika.

Anthu ena akufuna kwabwino ndi omwe anatengera bamboyu ku chipatala cha Cape Maclear atamva kufuula kwa mkuluyu kaamba ka ululu.

Powona kukula kwa bala la mkuluyu, chipatala cha Cape Maclear chinatumiza mkuluyu ku chipatala cha Monkey Bay komwe bamboyu akulandirabe thandizo la mankhwala mpakana lero.

Patricia Wyson yemwe akuyembekezeka kukaonekera ku khothi komwe akayankhe mlandu ovulaza munthu, ndiwochokera m’mudzi mwa Kwitumbi m’dera la mfumu yaikulu Chamba m’boma la Machinga.

Follow us on Twitter:

Advertisement