Zibwana zofinyana pakhosi: nthabwala za Ichocho zikhumudwitsa a Malawi

Advertisement

…apolisi awayendere — katswiri wa chitetezo

Ena akukanika kuyankhula momasuka chifukwa akuopa kukupidwa makofi. Ena ndiye angomasula. Koma a Malawi ochuluka aoneka odabwa ndi vidiyo imene watulutsa phona wa mu mzinda wa Blantyre, Ichocho, yolengeza kuti wayamba kufwamba anthu.

Malinga ndi kanema amene anthu akugawana, Ichocho ndi gulu lake la ziphona akhala ngati zigawenga za upandu za ISIS kapena Bokho Haram ndipo akulengeza kuti iwo akufuna azitengedwa ngati gulu la asilikari a nkhondo a dziko lino.

Iwo akuuza mkulu otchuka poyimira anthu pa milandu a Jai Banda kuti asunga mwana wawo Tonderai pa ukapolo mpaka a Banda atamenyera ufulu a Ichocho ndi gulu lawo kuti akhale odziwika ngati asilikari.

“Tamupanga kidnap mwana wanu a Jai Banda,” Ichocho akutero atazunguliridwa ndi anyamata ake omwe nawo ndi ziphona. “Timutulutsa mukatimenyera ufulu.”

Pamene kanemayu anatuluka, anthu sanazindikire kuti awa ndi macheza ndipo anthu ena anayamba kugwidwa nthumanzi. Koma Malawi24 yatsimikiza kuti izi zinali chabe nthabwala.

Koma poyankhula ndi Malawi24, katswiri poona nkhani za chitetezo amene anapempha kuti tisamutchure adanena kuti kanemayu ndi wa chibwana ndipo samayenera kutulutsidwa ndi kampani yopereka chitetezo.

“Apangazi ndi zodzetsa chisokonezo ndipo ndi mlandu ndithu,” anatero mkuluyi.

Iye anaonjezerapo kuti nthambi za chitetezo mu dziko muno zikuyenera kuyendera a Ichocho ndi kuwaphunzitsa khalidwe.

“Mukaona kanemayu akukhala ngati aja amatchedwa ma propaganda video a ISIS kapena kuti Boko Haram. Anthu akaona zotere amakhala ndi nkhawa, akufunika kudzudzulidwa kwa mphamvu ndi akulu akulu a za chitetezo,” katswiriyu anatero.

Iye anaonjezerapo kuti kupanga kanema otereyu pamene mayiko ena ngati Nigeria ndi Mozambique kuli mchitidwe otere ndi kusewera pa ulimbo.

“Atha kupangitsa ena kutengerapo mwayi. Ndipo pomafika poziyenereza ndi asilikari a dziko lino ndi kunyanzitsa asilikari athu,” anaonjezerapo.

Follow us on Twitter:

Advertisement