Kwavuta ku South Bend ku Amereka: Lulu akumusunga ngati nkhuku

Advertisement

…akushopa pa kaunjika wa kumeneko

Kumudzi kuno Lulu ndi namandwa oyimba. Zithunzi zake za makabudula pamene ali ku Amereka zikuoneka za mtengo wa patali. Koma oyimba Jolly Bro kapena kuti JB ati tisatengeke nazo. Ku Amereka, akutero ndi JB, Lulu akungomusunga ngati chiweto ku mpanyira wa kumeneko. Ndiponso ati olo kokashopa ndiye ndi ku kaunjika ndithu.

Mpungwepungwe wabuka mu dziko la Amereka kumene a Malawi aukirana pa nkhani ya show ya nyimbo imene ikuyeneka kuchitika kumeneko. Izi ndi malingana ndi oyimba nyimbo za chamba cha hip-hop Jolly Bro amene anamanga maziko ku USA.

Polankhula pa tsamba lake la mchezo la Facebook, JB wafotokoza kuti iye amapanga dongosolo loti achite show ya nyimbo kuti atolere ndalama zothandiza anthu amene anakhudzidwa ndi Cyclone Freddy. Iye wati mu dongosolo lake amafuna ayimbe ndi anthu ena a ku Amereka komweko. Koma pamene anayamba kuchita dongosolo lake, ena anamuuza kuti aonjezereponso Lulu kamba koti naye adakali mdzikolo.

Malinga ndi JB, iwo atafuna kuonjezera Lulu, anauzidwa kuti apemphe chilorezo kwa abusa a Kate Joyo amene ndi m’Malawi amene amakhala ku Amereka komweko ndipo ndi amene anayitanitsa Lulu. Atinso mayiwa pamodzi ndi mchimwene wawo Mahara Mhango ndiwo akusunga Lulu kunyumba kwawo.

Zikuoneka kuti poyamba anthuwa anagwirizana koma abusa a Joyo ndi mchimwene wawo Mahara anawona ngati kuchita show ndi JB sadyelera. Iwo anaitchola ndipo mmalo mwa JB, anayikapo Tay Grin kuti ndiye akayimbe ndi Lulu.

JB waonjezeranso kunena kuti mmalo moti ndalama za ku show zipite kwa anthu okhudzidwa ndi napolo wa Freddy, abusa a Joyo ndi achimwene awo agwirizana kuti azigawane.

“Ngati umapemphera kwa abusa amenewa ndiwe munthu opusa,” anakalipa chomwecho JB. “Ndi munthu oipa kwambiri ameneyu ndipo ndi wachinyengo.”

Ukali wa JB unasefukira pamene anauluranso kuti oyimba otchuka Lulu akungosungidwa ngati chiweto moti mdima ukagwa akumamusekera. Malinga ndi JB, anthu akukanika kumuonetsa malo osiyanasiyana Lulu chifukwa akumayenera kupempha chilorezo kwa abusa a Joyo.

JB wati mmalo moti Lulu akanamupezera malo ku hotela kapena ku lendi koti azitha kuzipangira zinthu yekha, iwo akumusunga mnyumba ngati mwana wa pakhomo ndi kumamupangira zochita.

“Lulu ndi munthu wamkulu, amafunika nyumba yake kapena ku hotela, osati kumamulera ngati mwana wa pa khomo iyayi,” anang’alura JB. Kenako anaulura kuti oyimba ambiri akapita kumeneku sikuti amalipiridwa molongosoka.

Iye anati malemu Martse atapita ku Amereka amangomumwetsa mowa mmalo momulipira. Ati Lulu anamutengera ku kaunjika wa ku Amereka kukagula zovala za mtengo otchipa.

“Osapita naye ku ma Mall a pamwamba bwanji?” anadabwa JB uku akukalipa kuti Lulu wangoshopa ngati akugwada pa msika wa ku Kawale.

Follow us on Twitter:

Advertisement