Namondwe wa Freddy: Phungu wa dera la Zomba Chingale wapempha thandizo

Advertisement

Phungu wa dera la Zomba Chingale Lonnie Phiri wati anthu a mu dera lake omwe akhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy akusowa zinthu zosiyanasiyana zofunika pamoyo wao watsiku ndi tsiku.

Phiri wauza Malawi24 kuti mdera la Zomba Chingale anthu pafupifupi 3,000 nyumba zawo zidagwa ndi mvula ya Namondwe ndipo akukhala m’malo anai (ma camp) komanso zinthu zawo zidakokoloka ndi madzi.

Iye wati anthuwa akusowa thandizo lachakudya, zofunda, zovala, ziwiya zophikira ndi zinthu zina.

Pamene Phunguyu wapempha Boma, mabungwe ndi anthu akufuna kwabwino kuti athandidze anthu okhudzidwawa popedza akukhala moyo wodzudzika pamodzi ndi ana awo.

Phiri wathokoza wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino Saulos Chilima chifukwa choyendera anthu amdera lake la Zomba Chingale omwe adakhudzidwa ndi Namondwe wa Freddy.

Phiri wapemphanso Bungwe la National Roads Authority (NRA) kuti liwakonzere mu mseu wa Zomba Chingale chifukwa wawonongeka ndi Namondwe wa Freddy.

Iye wati kuwonongeka kwa mseu umenewu kupangitsa kuti anthu a mdelari adzivutika kupita kuchipatala akadwala komanso maphunziro ndiye kuti alowa pansi mdera lake.

“Dera la Zomba Chingale lili pakati pamapiri choncho madzi ataphulika kuchokera ku mapiri adawononga miseu yonse pamodzi ndi milato choncho mayendedwe akukhala ovuta kwambiri,” adatero Mai Lonnie Phiri.

Poyankhulanso, wapampando woona zachitukuko mdera la Zomba Chingale a Redson Suman wati Namondwe wa Freddy wabweretsa umphawi kwa mabanja ochuluka popeza chimanga chawo, komanso nyumba zawo zidapita ndi madzi.

Suman wati ana a school ali pa chiwopsezo choti mayeso sachita bwino popeza sakumawerenga chifukwa mabuku awo adapita ndi madzi. Iye watinso pakhala povuta kuti galimoto zothandidza anthu ndichokudya zidzifika mdera la Zomba Chingale popeza miseu yawonongeka.

Advertisement