Atangwa kuvundukula ma siketi uku mmalo mokonza chuma: mzimayi wayalutsa Gwengwe

Advertisement

Bodza lonamiza dziko kumati mafuta atsika mtengo mu December lija ati amapitilira nalo. Ati amanamizanso amayi osiyanasiyana amene tikunena pano ndi oyembekezera. Anawaimikawo ati ndi a nduna ofatsa aja a Sosten Gwengwe.

Munthu wina wamayi wavula gule pagulu atabwera pa tsamba la mchezo la Facebook kufotokoza kuti iye wakhala akuzemberana ndi nduna ya za chuma a Sosten Gwengwe amene akukanika kukonza chuma cha dziko.

Malinga ndi mmayiyu amene akuzitchula kuti ndi Florie Cht pa Facebook, wati iye wakhala ali mu chikondi chozemberana ndi a Gwengwe kwa nthawi ndithu. Iye wati a Gwengwe adamulonjeza zinthu zochuluka koma alephera kukwaniritsa ngati a Tonse Alliance.

Pofuna kuonetsa kuti iye sakungolubwa, Florie wabwela ndi ma lisiti a ma screenshot oonetsa kuti iye ndi Gwengwe akhala ali mu chibwenzi ndithu.

Ena mwa ma lisiti amene wabweretsa mmayiyu ndi okhudza mphatso zimene a Gwengwe akhala akumugulira monga zikwama ndi nsapato. Akalandira mphatso izi iye amathokoza kwinaku nkuti akulonjezana chikondi cha mpaka muyaya ndi a Gwengwe amene ndi okwatira.

Mmayiyu wabweretsanso kugulu zithunzi zimene anajambulitsa ali ndi a Gwengwe, onse chimwemwe chili mtsaya ngati ana akakhuta mango akuba.

Pa mauthenga osinthana pa makina a mchezo a WhatsApp, munthu amene akunenedwa kuti ndi Gwengwe akulonjeza mkaziyo kuti iye akhala naye mpaka muyaya bola naye apitilize kumukonda.

Kuphatikiza ma lisiti amene wabweretsa mmayiyu, iye waonjezerapo kulemba kuti Gwengwe ndi oyendayenda ndipo mmalo mogwira ntchito yokonza chuma amakhala otangwa ndi zinthu zadama.

Mmayiyu waopseza kunena kuti iye azikhwedza chifukwa zochita za Gwengwe zikumupsetsa mtima.

Sizikudziwika ngati zimene akukamba mmayiyu ndi zoona kapena wasemera chinyau a nduna a Gwengwe.

Advertisement