Tikufuna nsima osati tchipisi, adandaula anthu kumisasa

Advertisement

Anthu ena omwe akhudzidwa ndi namondwe wa Freddy ndipo akukhala mmalo oyembekezera, awuza anthu akufuna kwabwino omwe akumakawazonda kuti asamawapititsire tchipisi ndi chiboda cha nkhuku, koma bolako nsima.

Izi ndi malingana ndi kanema amene anthu akugawana m’masamba a nchezo amene akuwonetsa mzibambo mmodzi okhudzidwa ndi namondwe wa Freddy akuuza mtolankhani wina kuti iwo sakufuna tchipisi kaamba koti sichikumawagwira mtima.

Munthuyu anamuuza mtolankhaniyo kuti chakudya chodalilika kwa iwo ndi nsima ndipo anthu omwe akumawayendera sakuyenera kumawagulira tchipisi ati kaamba koti sakumakhuta.

“Ndi nsima imene timadalira ife, asamatibweretsere tchipisi, ife tikufuna nsima. Tchipisi ndi chicken (nkhuku) palibe chikuchitika, azitibweretsera nsima ya chi Malawi. Kapena azibweretsa phala la mpunga ndilabwino kapenaso phala la mgaiwa ndilabwinoso koma osati tchipisi ndi nkhuku,” watelo munthuyo.

Nkhaniyi yabweretsa mtsutso pakati pa anthu kaamba koti ena akuti anthu amene ali mmalo oyembekezera potsatira madzi osefukira, sakuyenera kumasankha zakudya koma akuyenera kumalandira zomwe zapezekazo.

Anthu ena akuikira kumbuyo mkuluyu ponena kuti, mfundo yake ndiyoveka potengera chikhalidwe cha a Malawi pomwe munthu akati wadya chakudya chenicheni, amanena nsima.

Chatsitsa dzaye kuti njobvu ithyoke mnyanga mchakuti zikumveka kuti Lolemba lapitali akuluakulu ena aboma anawagulira anthu okhudzidwa ndi madzi osefukirawa omwe anali pa nsasa wina mumzinda wa Blantyre tchipisi komaso kachiboda ka nkhuku.

Follow us on Twitter:

Advertisement