A Joyce Banda akuwonelera zisankho m’dziko la Nigeria

Advertisement

Mtsogoleri wakale wa dziko la Malawi a Joyce Banda ali m’dziko la Nigeria komwe akutsogolera nthumwi 40 zochokera maiko osiyana siyana padziko lonse kuwonelera zisankho zomwe zikuchitika m’dzikolo.

Banda wauza Malawi24 kuti mabungwe a National Democratic Institute (NDI) ndi International Republican Institute omwe ndi aku United States of America ndiwomwe adamupempha kuti atsogolere nthumwi 40 zochokera ku Asia, Europe, North ndi South America komanso zochokera kuno ku Africa.

Iye wati popeza dziko la Nigeria ndi lalikulu kwambiri, nthumwizo ziwonelera zisankhozo mu madera 20 mwa madera 36 omwe ali m’dzikolo ndipo wati chitetezo chilipo chokwanira ndipo konse komwe akupita akutsogoleledwa ndi asilikari.

“Ndilikuno ku Nigeria komwe ndikutsogolera nthumwi 40 zochokera padziko lonse lapansi motumidwa ndima Institutions a NDI komanso IRI omwe ndi aku America ndipo zonse zikuyenda bwino madera onse omwe tikuyendera.” Adateto Dr Joyce Banda.

Mtsogoleri wakale wadziko linoyu wati wakumananso ndi yemwe akutsogolera nthumwi zomwe zikuwonelera zisankho zochokera ku bungwe la European Union. Iye watinso wakumana ndi President wa bwalo a High Court wa dziko la Nigeria kukambirana momwe angayendetsere milandu yachisankho ngati pangapezeke wina okadandaula.

Mu dziko la Nigeria mukuchitika chisankho chomwe anthu am’dzikolo akusankha mtsogoleri watsopano.

Anthu mu dzikolo anaponya voti dzana ndipo pakali pano kuwerenga mavoti kuli mkati.

Follow us on Twitter:

Advertisement