Aphungu avala ziguduli ku nyumba ya malamulo

Advertisement

Kunali chipwilikiti ku nyumba ya malamulo lero pomwe aphungu otsutsa boma anavala mayekete, madilesi ndi mabuluku opangidwa kuchokera ku masaka ati pokwiya ndi ulamuliro wa Lazarus Chakwera.

Malingana ndi aphungu ena, iwo anaganiza zovala ziguduluzi ngati njira imodzi yowonetsa kusakondwa kwawo ndi omwe mtsogoleri wa dziko lino a Chakwera akuyendetsera boma ponena kuti zinthu zambiri sizili bwino.

A phungu otsutsa bomawa anapeleka zitsazo zakusayenda bwino kwa chuma chadziko lino, kukula kwa mchitidwe wa katangale ndi ziphuphu, kukwera kwa katundu osiyanasiyana komaso kulephera kuyendetsa bwino ndondomeko yazipangizo zotsika mtengo ya AIP zomwe akuti zipangitsa dziko lino kukhala pa njala ya dzaoneni.

Izi zinabweretsa mtsutso waukulu m’nyumbayi kaamba koti aphungu a mbali ya boma amafusafusa ngati kunali koyenera kuti aphungu otsutsa bomawa avale ziguduli ngati momwe anapangira.

Phungu wadera la kum’mwera kwa boma la Ntchisi a Ulemu Chilapondwa omwe ndi achipani cha Malawi Congress (MCP), anapeleka dandaulo kwa sipikala wanyumbayi a Catherine Gotani Hara kuti awunikelepo pa mavalidwewo.

Aphungu ku nyumba ya malamulo

Ndipo poyankhapo pa pempholo, a Hara analamura kuti aphungu omwe avala ziguduliwo asapezeke nawo pakutsekulira kwa nyumba ya malamuloyo ponena kuti gawo 204 ya malamulo a mnyumbamo, aphungu amayenera kuvala zovala zabwino.

Koma ganizoli linakumana ndi mtsutso waukulu kuchokera kwa aphungu ambali yotsutsa boma ndipo wachiwiri kwa mkulu osungitsa bata kumbali yaboma a Khumbize Kandodo Chiponda anapempha a sipikala a Hara kuti nkhaniyi isawatayitse nthawi.

A Chiponda anati tsikuli lotsekulira nyumba ya malamulo ndilalikulu choncho nkufunika kuti nkhaniyi ayipititse ku komiti yoona zamalamulo m’nyumbayi kuti ayiwunikire bwino mtsogolo muno.

Apa a Hara analamula kuti aphungu otsutsa boma omwe anavala ziguduliwo, atha kukhala nawo pakutsekulilidwa kwa nyumba ya malamuloyo ndipo nkhaniyi ayipeleka ku komiti yowona za malamulo mnyumbayi kuti akayiwunike bwino.

Ena mwa aphungu omwe avala ziguduli ndi monga phungu wadera lapakati m’boma la Thyolo a Ben Phiri, Phungu wadera la kumadzulo kwa boma la Mulanje a Yusuf Nthenda, kungotchulapo ochepa.

Follow us on Twitter:

Advertisement