Mtsogoleri wakale wa dziko lino a Peter Mutharika ati a pulezidenti Lazarus Chakwera akanika kuyendetsa boma ndipo pali tsogolo lakuti chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) chibwerera mu boma.
A Mutharika amayankhula izi dzulo ku msonkhano omwe anachititsa ku St Augustine 3 Primary School Ground mu boma la Mangochi.
Malingana ndi a Mutharika, zinthu mdziko muno sizikuyenda bwino ndipo mitengo ya katundu wambiri yakwera pansi pa ulamuliro wa a Chakwera.
Iwo anaonjezera kuti ku Malawi kuno kuli njala komanso kulibe fetereza ndi ndalama zakunja. Apa a Mutharika anati iwo anasiya ndalama zakunja zokwana ma dollar 1.1 biliyoni koma pano zonse palibe.
Iwo anadzudzulanso boma la Chakwera posapitiriza zitukuko zomwe boma la Mutharika limachita monga pulogalamu ya malata ndi simenti zotchipa yomwe anati limathandiza anthu ovutika.
“Boma lawakanika komanso kuyendetsa chuma kwawakanika. Mitengo ya zinthu yakwera ndi a Chakwera,” anatero a Mutharika.
Apa a Mutharika anati chipani cha DPP ndi chokonzeka kubwereranso mu boma mu 2025 kuti chikonze dziko lino.
“Ndikupempha anthu onse mu Malawi muno kuti bwerani ku DPP. Ife tatsegula khomo lero kuti tonse tigwirizane kuti tisinthe dziko lino. Kuti mavuto omwe alipowa athe, ndipofunika kuti tonse tigwirizane,” anatero a Mutharika.
Iwo anamemanso onse amene anatuluka chipani cha DPP kuti abwerere ndipo adzalandilidwa.
Follow us on Twitter: