A Kalindo ati akachita nawo zionetsero

Advertisement

Pamene oyankhula pa fesibuku Joshua Chisa Mbele yemweso ndi mmodzi mwa akuluakulu abungwe la Citizens Against Impunity and Corruption waitanitsa zionetsero sabata yamawa, Bon Kalindo yemwe mmbuyomu analankhula kuti ‘a Malawi siowafela’ wati akachita nawo zionetserozo.

Kumayambiliro kwa sabata ino, Chisa Mbele walengeza kuti Lachinayi sabata yamawa pa 27 October, kukhala zionetsero za dziko lonse zomwe waitanitsa mogwirizana ndi magulu ena pankhani yakusokonekera kwa zinthu mdziko muno.

A Mbele omwe analemba patsamba lawo la fesibuku anati zionetserozi ndinjira imodzi yowonetsa mkwiyo ndikubedwa kwa K30 biliyoni ya fetereza otsika mtengo, kusowa kwa mafuta a galimoto, kusowa kwa ndalama zakunja komaso mankhwala mzipatala.

Iwo anatiso ndizokhumudwitsa kuti mchitidwe wa ziphuphu ndi katangale ukuchulukirabe mdziko muno ndipo ati chokhumudwitsa kwambiri mchoti atsogoleri ena aboma akukhudzidwa nawo ndipo ati zionetserozi ndizofuna kupulumutsa dziko lino lomwe iwo ati likutayika.

“A Malawi onse kuchokera ku Nsanje mpaka ku Chitipa agwirizana chinthu chimodzi. Tilibe boma. Tili ndi mbava zomwe zikudzithandiza zokha pa tizinthu tathu tochepa tomwe tili nato.
Tiwatengera a Malawi ku nyumba ya chifumu chifukwa tikukhulupilira kuti ndi komwe za katangalezi zimayambira.

“Anakakhala kuti a Chakwera sakukhudzidwa, katangale anakatha. Anakakhala kuti a Chakwera sakukhudzidwa, ACB bwezi itachita zolozeka. Anakakhala kuti a Chakwera sakukhudzidwa, mabwalo a milandu anakafulumizitsa milandu ina. Anthu Otopa, Oberedwa, Opanda Mafuta, Osowa Pogwira, tikamuyendere Chakwera,” atelo a Mbele pa tsamba lawo la fesibuku.

Kuitanitsidwa kwa zionetselozi kwasangalatsa anthu komaso magulu ochuluka kuphatikizapo bungwe la Forum for National Development (FND) lomwe kudzela mumchikalata chomwe latulutsa chosayinidwa ndi a Fryson Chodzi, lati likapanga nawo zionetselozi.

Koma chadabwitsa anthu ambiri mchoti a Bon Kalindo omwe mmbuyomu analengeza kuti zazionetsero azitaya, ali nawo kalikiliki kumemeza anthu kuti akatenge nawo gawo pa zionetserozo sabata yamawa ponena kuti zinthu sizili bwino mdziko muno.

Makanema angapo omwe anthu akugawana mmasamba anchezo, a Kalindo awuza anthu kuti omenyera maufulu mdziko muno agwirizana kukachita zionetserozi ndipo ati boma la Tonse lidzatuluka m’boma ndi zionetsero poti nalo linalowa ndi zionetsero zomwezo.

“Ngati uli ndi vuto la feteleza, tsiku lokalandira yankho ndi pa 27 October. Wina ngati akutenga ndalama zaboma kumawapatsa ana ake, tsiku lamayankho ndi pa 27 October. Ngati ulidi m’Malawi weniweni ndipo umafunira dziko lako zabwino, tsiku lake ndi pa 27 October.

“Oyenda ndilupanga, ndilupanga lomweloso lomwe lidzamuphe. Chomchoso amene analowa m’boma ndi zionetsero, zionetsero zomwezoso ndi zomwe zidzamutulutse m’bomamo. Osaopa, tiyeni a Malawi tonse tituluke,” atelo a Kalindo.

Izi zakhumudwitsa anthu ena omwe akuti sakufuna mkuluyu akhale mugulu lotsogolera zionetserozi ponena kuti samachedwa kusintha mawanga ndipo ena ati ngati a Kalindo angakhale nawo patsogolo kutsogolera zionetserozi, satenga nawo gawo.

“Mneneri kumulora winiko is adding salt to our wounds (ndi kuthira mchele pamabala athu). Ndichimodzimodzi kutiuza kuti a nduna a Mtambo akakhala nao pamwambowo,” anatelo a Francesca Banda poyikira ndemanga pa tsamba la Chisa Mbele.

Nawo a Racheal Kudzala anati; “Komatu a Yoswaaaa muli Phuma lanyooooo. Basi over a sudden (mwadzidzi) mwajoyinisa a Winiko. Koma zina inu, zatigwesa ulesi izi. Mukapange ndachambuyanu, ife bora tisamire pa Yesu.”

Pakadali pano anthu mmasamba a amchezo akugawanaso kanema ina yomwe Kalindo akuoneka ataima ndi mzimayi wina ndipo anayankhula kuti; “a Malawi siowafela, umayenera munthu uzipanga zako zoti zikuthandize kuti upeze makobidi.”

Follow us on Twitter:

Advertisement