Mlendo ndimame sachedwa kukamuka: Mneneli Mbewe watuluka PP

Advertisement

Pomwe anthu otsatira chipani cha People’s (PP) anali ndi chimwemwe chodzadza tsaya kuti mwina mkutheka Mneneli David Mbewe awatengera mtsidya lina, munthu wa Mulunguyu watuluka mchipanichi atakhalamo maola ochepa.

Mneneli Mbewe analowa chipani cha PP lachinayi pa 11 August ndipo mwambo omulandira mkuluyu unachitikira mu mzinda wa Lilongwe komwe akuluakulu achipani cha PP anati ndiosangalala kaamba kachisankho cha mlendoyo.

Pakutha pamwambo olandira a Mbewe kukhala membala wa chipani cha PP, ofalitsa nkhani mchipani cha PP, a Ackson Kalaile Banda, anauza atolankhani kuti a Mbewe athandiza kupititsa patsogolo ntchito za chipani chawo m’dziko muno.

Mneneli David Mbewe ndi m’modzi wa anthu omwe anali wotsatila chipani cha Democratic Progressive (DPP).

Koma chisangalalo chili mkati ndipo patangopita maola osaposera asanu ndi awiri (7), Mneneli Mbewe walengeza kuti watuluka m’chipani cha PP chomwe analowachi.

Malingana ndi chikalata chomwe a Mbewe atulutsa, iwo apanga chiganizo chotuluka mu PP kaamba koti chipanichi chalephera kukwanilitsa mfundo zina za mgwirizano omwe anapangana iwo asanalowe mchipanichi.

A Mbewe omwe amatsogolera mpingo wa Living Word Evangelical, ati iwo pamodzi ndi akulu akulu achipani cha PP, anagwirizana kuti iwo akangolowa mchipani cha PP, nthawi yomweyo chipanichi chituluka mu mgwilizano wa Tonse.

Iwo ati ndiodabwa kuti atalowa mchipanichi, PP sinatuluke mumgwirizano wa Tonse ndipo ati chatsitsa dzaye kuti apange chisankho chotuluka m’chipanichi nchakuti anapatsidwa udindo ku imodzi mwa makampani a boma.

“Mfundo yaikulu inali yoti PP ituluke mu mgwirizano wa Tonse. Choncho ndi m’mene zililimu ine ndilibe chochita china kupatula kukhala mbali ya a Malawi. Ine ndadabwa kuti patangotha mphindi zochepa nditalandilidwa, ndinapatsidwa udindo ku bungwe lina la boma.

“Ine ndi munthu amene ndili ndimfundo zanga zomwe ndimatsatira nthawi zonse ndipo sindingakhale nawo mugulu lochita zinthu izi,” watelo mneneri Mbewe pomwe amatuluka chipani cha PP.

Zonsezi zikuchitika pomwe mneneli Mbewe posachedwa anawonetsa chidwi chachikulu chodzapikisana nawo pampando wa mtsogoleri wa chipani chotsutsa boma cha Democratic Progressive Party (DPP).

Follow us on Twitter:

Advertisement

2 Comments

Comments are closed.