Anthu ochuluka mdziko muno akupitilira kukakamiza nduna yowona za mphamvu ya magetsi a Ibrahim Matola kuti abwere poyera ndikupepesa kaamba konena kuti anthu omwe akudandaula kuti Lazarus Chakwera akuyendayenda kwambiri ndi achule.
Mosalingalira kuti kunena kwa ndithe ndithe nanthambwe anazitengera, a Matola anayankhula izi Lolemba pa 6 June ku Golomoti m’boma la Dedza komwe mtsogoleri wa dziko linoyu amakhazikitsa ntchito yapanga mphamvu yamagetsi kuchokera kudzuwa.
Ndunayi inauza a Chakwera pamwambowu kuti asavere anthu omwe akudandaula za kayendedwawa ndipo mobweleza bweleza iwo anati anthu omwe akuletsa mtsogoleri wadzikoyu kuyendayenda ndi achule.
“Posachedwaoa apulezidenti mukhala mukuyenda, ndiposo tisawavere achulewa amene akunena kuti osamayenda, osamayenda,” anatelo Matola.
Koma patangodutsa maola ochepa ndunayi itayankhula chipongwechi, anthu oyankhula pazinthu zosiyanasiyana komaso a Malawi ena makamaka m’masamba amchezo, adzudzula ndunayi kaamba koyankhula mowola pakamwa.
Mkulu wa bungwe la Center for Mindset Change (CMC) a Phillip Kamangirah kudzera mumchikalata chomwe atulutsa, ati zomwe ayankhula a Matola ndimwikho komaso mwano kwa a Malawi omwe ati amapeleka ndalama zowalipira andunawo kudzera ku misonkho.
A Kamangirah kudzera mumchikalatachi ati ndipofunika kuti ndunayi ipesese kaamba kamawu ake onyozawa ponena kuti izi sizimayenera kuyankhulidwa ndi munthu waulemu wake ngati momwe alili iwowo.
“Mau awa ndioyipsa umunthu, ndiosaloledwa pandale, ndiolakwika paulemu ndipo pamwamba pazosezi sakuyenera kuyankhulidwa ndi nduna yomweso imalandira ndalama kuchokera kwa a Malawi omwe lero akuti ndi achulewo.
“Ngati bungwe lowona zaulamuliro wabwino, tikuwapempha bambo Ibrahim Matola kuti apepese kwa a Malawi kaamba kamawu awo. A Matola kuyenera kudziwa kuti udindo wawo waundunawo ndiwoti atumikile anthu aku Malawi osati achule,” atelo a Kamangirah mumkalatayo.
Chikalatachi chalangizaso aphungu onse anyumba ya malamulo mdziko muno kuti asiye mtchitidwe odzimva kuti afikapo, ponena kuti malipilo omwe aphunguwa amalandira ndi ndalama zomwe a Malawi amazipeza movutikira choncho sibwino kunyoza owalipira.
Pophera mphongo pa izi, m’modzi mwa anthu omenyera ufulu mdziko muno a Luther Mambala, ati zomwe ndunayi yanena ndi chitonzo kwa a Malawi omwe adavotera boma la mgwirizano wa Tonse.
A Mambala ati pofuna kupereka phunziro kwa nduna zina, mtsogoleri wadziko lino akuyenera kupeleka mwambo kwa a Matola powachotsa paudindo wawo wa unduna.
Mbali inayi, anthu ena omwe anathilira ndemanga pankhaniyi yomwe inaikidwa patsamba lino Lolemba masana, ati ndiokwiya ndi zomwe ayankhula a Matola ndipo ambiri mwaiwo anati mkuluyu akuyeneradi kupepesa.
” Mr Matola kulankhula kwabwanji uku..Tonsefe ndi AMalawi..Chonde muziganiza bwino musanalankhule..Mwayiwala kale kuti ine tonsenu AMalawi amakulupirana ndalama zawo zaMisonkho,” anatelo a Hamiton Solomon.
Nawoso a Oliver Nyamam’mbare anati: “Mr president mudziwe kuti nduna yanu yukunamizani pomakuuzani kuti dziko likuyenda bwino. Mr Usi sadalakwe anthu monga awa achotseni ntchito.”
Pakadali pano anthu mmasamba amchezo akugawana mbali yakanema yazomwe a Matola ayankhula ndipo ena akugawanaso chithuzi chomwe chikumaonetsa ndunayi mbali ina kuli achule.
Follow us on Twitter: