Chakwera, Chilima akukaipatsa moto Flames

Advertisement

Mtsogoleri wa dziko lino Lazarus Chakwera, pamodzi ndi wachiwili wake Saulos Chilima, alengeza kuti akaonera nawo mpira wapakati pa timu ya dziko lino ndi Ethiopia pa bwalo la Bingu lamulungu lino.

Izi ndimalingana ndi chikalata chomwe boma latulutsa lachisanu chomwe chimafotokoza mndandanda wamomwe a Chakwera agwilire ntchito kumathero a sabatayi komaso kumayambiliro a sabata ya mawa.

Mbali inayi, naye wachiwiri kwa mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima, nawo kudzera kwa ofalitsa nkhani wawo Pilirani Phiri, alengeza kuti akakhala ali pa bwalo la masewero la Bingu, uku akuchemelera timu yadziko linoyi.

Izi zabweretsa chimwemwe kwaotsatira masewera a mpira wamiyendo ambiri omwe akuti kupezeka kwa atsogoleri adzikowa kumasewerowa kupeleka nyonga zapadera kwa osewera mu timu yadzikoyi.

Awa ndi masewero oyamba a timu yadziko linoyi pomwe matimuwa akudzigulira malo mumpikisano wa African Cup of Nations (AFCON) omwe uchitikile mdziko la Ivory Coast chaka chamawa.

Follow us on Twitter:

Advertisement