Chikho cha AFCON chalandiridwa mopatsa chidwi ku Senegal

Advertisement

Wolemba: Gracious Zinazi

Anthu mazanamazana anadzadza mu misewu ya mu mzinda wa Dakar ku Senegal dzulo kukalandira osewera a timu ya dziko lawo omwe atenga chikho cha AFCON.

Tsiku la 6 February 2022 ndilosaiwalika kwa mzika za dziko la Senegal chifukwa team ya dzikoli inagonjetsa Egypt mu mpikisano wa African Cup of Nations ku Cameroon kudzera ma penate.

Mtsogoleri wadzikoli Macky Sall sadachitire mwina koma kubwerera pa ulendo wake opita kunja kwa dzikoli ndicholinga chofuna kuzalandira osewera omwe afika dzulo pa 7 February. Sall analamula kuti dziko lonse lipange tchuthi ngati njira yolandira komanso kusangalala kuti osewerawa apambana.

Bus yomwe anakwera osewerawa inayenda pang’onopang’ono kuchokera ku bwalo la ndege kukafika kunyumba ya mtsogoleri wadzikoli komwe anawakonzera m’gonero chifukwa misewu inadzadza ndi anthu omwe amaimba nyimbo zotamanda timuyi mosalekeza.

Polankhulana ndi tsamba la intaneti la France24, ena mwa masapaotawa amati akhala akudikira kwa zaka zambiri kuti awone timu yawo itawina chikho cha AFCON.

Aka ndi koyamba Senegal kutenga chikhochi koma inafikakonso mu ndime yotsiliza mu 2002 ndi mu 2019 pomwe inaluza.

Mpikisano wa AFCON umachitika pakatha zaka ziwiri ndipo wina uchitika mu chaka cha 2023 m’dziko la Ivory Coast.

 

 

 

 

Advertisement