Katemera 210,000 wa Covid atha mphamvu pakutha kwa chakachi

Advertisement
Wachiwiri kwa wapampando wa gulu lowona za Covid19, a Wilfred Chalamira Nkhoma, ati katemera 210,000 akhala atatha mphamvu pakutha kwa chakachi.
Iwo amayankhula izi pa msonkhano omwe bungwe la madotolo linakonza kudzera pa njira ya Zoom.

Iwo anati katemera ali ndi nthawi yochepa ndipo amatha mphamvu mwamsanga. Izo ndizo zinawakakamiza kuyamba njira yopita khomo ndi khomo kuti anthu abayitse katemera.

A Nkhoma anali m’modzi mwa gulu lomwe linalipo pa zokambilanazi, zomwe anthu okhudzidwa omwe ndi  nzika zaku Malawi koma zikukhala kunja zimafuna kudziwa zitamva kuti katemera 700, 000 atha mphamvu pakutha kwa chakachi.

A Daniel Dube anafusa kuti chifukwa chiyani katemera atha mphamvu pomwe akufunidwa kwambiri, ndipo poyakhapo a Nkhoma anati katemera ndiwosakhalitsa kumangomusunga komanso anati zikhulupiliro zina za anthu ndizomwe  zikupangitsa kuti anthu ambiri asabayitse.

Apo ndi pomwe katswiri owona zamatenda opatsirana a James Chiphwete anapereka maganizo kuti dziko lino liyenera kuyambitsa njira yobwedzeletsa masiku oti mankhwala atsungike monga momwe ku United Kingdom amapangira.

Pulezidenti wama dotolo mdziko muno a Victor Mithi anati boma liyenera kuchilimika kuti anthu ambiri abayidwe, iwo anati bungwe lawo linapanga kafukufuku ndipo linapeza kuti anthu samamvera zomwe azaumoyo amanena ponena kuti anthu amakhulupilira kuti azaumoyowa akutumidwa kuti achepetse chiwerengero cha anthu.

“Anthu akuwoneka kuti sakumvesabe za Covid19 ndipo sali okonzeka kutenga katemera , koma tikuyenera kuti anthu amvetse za izi kuti nkhondoyi tiwone” anatero a Minthi.

Boma la Malawi likuyembekeza kuti nzika pafupifupi 11 million atenge katemera. Kufikira lero anthu 69,735 ndi omwe adwalapo Covid19.

 

 

 

Advertisement