Mtsogoleri wa dziko lino la Malawi a Lazarus Chakwera wadzudzula mchitidwe wa anthu ena osagwira ntchito kaamba kodalira thandizo lochokera kwa anthu andale ponena kuti mchitidwewu ukukolezera khalidwe loba ndalama zaboma.
A Chakwera amayankhula izi lolemba ku BICC mumzinda wa Lilongwe komwe amakhazikitsa gawo loyamba la zaka khumi la masomphenya a dziko lino pofika chaka cha 2063.
Iwo anati anthu akuyenera kumagwira ntchito kuti azizipezera zinthu zomwe akufuna pamiyoyo yawo komaso kudyetsa mabanja awo osati kumadalira kulandira thandizo kuchokera kwa anthu andale
Mtsogoleri wa dziko linoyu anatiso sibwino kuti anthu andale apitilire kumapereka zinthu kwa anthu ati kaamba koti izi zimapangitsa kuti andalewa akhale ndimalingaliro okaba ndalama zaboma zomwe anena kuti mzobwezeretsa chitukuko.
A Chakwera anapeleka chitsanzo chaiwo kuti pali anthu ena ambiri omwe amawatumizira mauthenga pa foni yawo kuwapempha thandizo la mabanja awo ndipo ati ena amafika pomawaopseza kuti ngati sawathandiza sadzawavotelaso.
“Sizowona kumanena kuti mesa tinakuvotelani, ndetu mpaka mauthenga ochita kuposa 500 ondiuza kuti ndiyendetse banja la aliyese kuchokera ku Chitipa mpaka ku Nsanje chifukwa choti ndine pulezidenti. Mpaka kumandiuza kuti mwatiyiwala eti? Mutifunatu.
“Pulani iyi kuti itheke mpofunika kuti inu andale muleke kunyengelera anthu ndi zinthu zowapatsa. Anthu andale mukuwapempha zinthu wa alibe kokatenga ndalama koma kukaba ku ofesi m’boma. Kodi tipitilire kumaba kuti inuyo mupitilire kupatsidwa zinthu zaulere?” Anatelo a Chakwera.
A Chakwera anaonjezera kuti anthu omwe amawatumizira mauthenga pafoni yawo asayembekeze kuti adziwayankha uthenga uliwonse ponena kuti ngati atakhala bize ndifoni, mapeto ake zitukuko zambiri sizichitika mdziko muno.
Iwo anatiso anthu asamangosilira kutukuka pa chuma kwa maiko ena monga South Africa komaso Rwanda ponena kuti anthu mmaikomo amadzipeleka kwambiri pogwira ntchito “osati zachibwana zomwe timachita kwathu kunozi ayi.”
Mtsogoleri wa dziko linoyu anatiso: “Okondedwa, azunguwa sangatikwezere dziko lino, pofunika tikweze tokha. Wina ochoka kwina sabwera kudzalima pamunda panu paja. Ofunika mukalime ndinu vula isanagwe. Aliyese agwire ntchito modzipeleka.”
Ndondomeko ya zaka khumi yomwe a Chakwera akhazikitsa ya Malawi 2063 first 10-year Implementation Plan (MIP-1), ikulosera kuti pofika chaka cha 2030 dziko lino lidzakhala lozidalira pachuma ndipo ndondomekoyi ikufuna ndalama zosachepera 15 billion za ku America
Yawechete bwenyeyo tutende