Chimodzi mwazipani zikuluzikulu mumgwirizano wa Tonse, UTM, chauza anthu mdziko muno kuti asiye kuyambitsa nkhani zomwe zitha kudanitsa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera ndi wachiwiri wawo a Saulos Chilima.
Nkhaniyi ikutsatira chithunzi chomwe chikuyenda pa masamba amchezo chomwe pali nkhope ya wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko lino Saulos Chilima ndipo palembedwa kuti momwe a Lazarus Chakwera ali kunja kwa dziko lino, wachiwiri wawoyu akuyendetsa bwino dzikoli.
Mwa zina zomwe anthu akuti zayenda bwino pomwe a Chakwera ali kunja kwa dziko lino ndi monga kulandira nsanga malipiro kwa ogwira ntchito m’boma omwe alandira ndalama zawo zamwezi uno Lachisanu pa 22.
Nkhaniyi yakwiyitsa akuluakulu achipani cha UTM omwe kudzera kwa oyankhulira chipanichi wamkulu a Frank Tumpale Mwenifumbo, nkhaniyi ndiyongofuna kudanitsa mtsogoleri wadzikoyu ndi wachiwiri wake.
Mu mchikalata chomwe chatulutsidwa Lamulungu, a Mwenifumbo ati a Chilima amagwira ntchito pansi pa ulamuliro wa a Chakwera ndipo ndikulakwitsa kunena kuti iwo agwira ntchito bwino kuposa mtsogoleri wa dziko lino.
“Ife ngati atsogoleri achipanichi tikufuna titsutse chithuzichi komaso zonse zomwe zakhala zikunenedwa mmbuyomu zofuna kubweretsa kusagwirizana pakati pa mtsogoleri wadziko Dr Lazarus Chakwera komaso wachiwiri wawo Dr Saulos Chilima.
“A Chilima amagwira ntchito yomwe awuzidwa ndi a Chakwera, choncho chilichonse chaboma chimachitika ndichilolezo cha mtsogoleri wadziko. Aliyese onena kuti chinthu chachitika ndimphavu zawina osati mtsogoleri wadziko, ameneyu ndi mbuli, sakudziwa mmene boma limayendedwetsera,” atelo a Mwenifumbo.
Mlembi wa UTM yu anaonjezeraso kuti anthu m’dziko muno akuyenera alemekeze a Chakwera kaamba koti dziko lililonse limakhala ndi mtsogoleri mmodzi panthawi ndipo ati kuwapatsa ulemu kutha kuthandiza kuti dziko lino lipite patsogolo pachitukuko.
Pomaliza, chipanichi chati chikudziwa kale anthu onse omwe akufuna kubweretsa udani pakati pa achakwera ndi a Chilima ndipo chaopseza kuti ngati sipakhala kusintha, chipanichi chichititsa manyazi anthuwa powaika pa mmbalambanda.
“Onse omwe ali ndi maganizo ofuna kudanitsa azitsogoleri athu mbali zonse, adziwe kuti tikuwaona, tiwayalutsa ndipo achititsidwa manyazi. Maganizo awo satheka chifukwa a Malawi sangalore zimenezo,” anaonjezera choncho a Mwenefumbo mumchikalatachi.