A Chakwera aluza mlandu: khothi lawalamula kulipira ndalama

Mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera aluza mulandu ku khothi ndipo khothi   lawalamula kulipira ndalama kaamba kofuna kubwezeretsa a Noah Dalasi Chasafali pa mpando wa mfumu yaikulu Ngabu mosatsata malamulo.

Nkhaniyi ikudza pomwe mtsogoleli wakale wa dziko lino a Peter Mutharika adachotsa pampandowu a Dalasi Chasafali kaamba kosasunga mwambo pa zinthu zina.

Ndipo atafusidwa kutelo, mafumu ena amdelari adapeleka kwa a Mutharika dzina la a Bisitole Dalitso Makwalu kwa a Mutharika kuti ndiwo akuyenera kukhazikitsidwa kukhala mfumu yaikulu Mgabu.

Potsatira kupambana pachisankho chachibwereza chaka chatha, a Chakwera analamura kuti a Dalasi Chasafali abwezeletsedwa pampando wa mfumu yaikulu Ngabu zomwe sizinasangalatse a Dalitso Makwalu.

Ndipo potsatira izi, a Makwalu anatengera nkhaniyi ku bwalo lamilandu lalikulu mumzinda wa Blantyre kuti chilungamo chidziwike ndipo chigamulo chankhaniyi chapelekedwa Lachiwiri pa 21 September, 2021.

Oweluza milandu ku bwaloli omwe ndi a Justice Mandala Mambulasa agamula kuti chiganizo chomwe a Chakwera adapanga chobwezeretsa a Dalasi Chasafali pa mpando wa mfumu yaikulu Ngabu, chinali chosatsata malamulo ndipo nchosalondola.

A Justice Mambulasa alamula oyankha mlanduwu omwe ndi mtsogoleri wa dziko lino, a Lazarus Chakwela komanso a Noah Dalasi Chasafali kuti alipila ndalama zonse zomwe zagwiritsidwa ntchito pa mulanduwu.

 

Ndipo yemwe amayimilira mbali ya odandaula a Michael Goba Chipeta ati zokonzekela zamwambo ofuna kukhazikitsa ngati mfumu yaikulu Mgabu a Basitole Dalitso Makwalu, zili mkati.

Pakadali pano, anthu m’masamba a mchezo ati pakuyenera pakhale kalondolondo wabwino pofuna kuonetsetsa kuti a Chakwera apereka ndalamazi kuchokera mthumba mwawo osati atenge misonkho ya aMalawi.

Posachedwapa, mtsogoleri wakale wadziko lino a Mutharika komaso amene anali mlembi wa boma a Lloyd Muhara alipira ndalama zokwana K69 million kaamba kotumiza kutchuthi oweruza milandu a Chief Justice Andrew Nyirenda komaso a Justice of Appeal Edward Twea.

Advertisement