Mlembi wa mkulu mum’chipani chotsutsa boma cha DPP a Grezelda Jeffrey anagwada m’bwalo lamilandu kwinaku akukhetsa misozi pomwe amapepesa nduna ya zamasewero a Ulemu Msungama powanena kuti anagwililira nsuweni wawo.
Nkhaniyi ikutsatira zomwe zinachitika chaka cha 2017 pomwe a Jeffrey anayankhula pansonkhano wa ndale kuwuza anthu kuti asavotele a Msungama ngati phungu wanyumba ya malamulo kaamba koti anagwililira nsuwani wawo.
Potsatira izi a Msungama anatengera nkhaniyi kubwalo lamilandu ponena kuti nkhaniyi ndiyabodza ndipo a Jeffrey akungofuna kuwaipitsira mbiri yawo.
Ataonekera kubwalo lamilandu Lachiwiri pa 24 July komwe zomwe anayankhula zinaseweredwa, mlembi wa DPP yu anagwada pansi ndikupepesa atagwira mwendo wa a Msungama pazomwe anayankhulazi kwinaku misozi ikutsikira m’masaya.
Ndipo poyankhapo pa kupepesaku, a Msungama awuza zina mwanyumba zofalitsira mawu mdziko muno kuti Iwo alandira kupepesaku ndipo anaonjezera kuti anali okondwa kuti mayi Jeffrey apepesa pazomwe anayankhulazi.
Iwo anati anatengera nkhaniyi kubwalo la milandu pofuna kuphunzitsa andale kuti asamakomedwe ndi kuyankhula nkhani zonyoza anzawo makamaka nthawi ya misonkhano yokopa anthu.
“Kugwada, kulira komaso kugwira mwendo mukhothi ngakhale kunali ngati sewero, koma ndinjira imodzi yomwe ife a Malawi timachita tikafuna kupepesa mosweka mtima ndipo ngati mmodzi mwa anthu omwe ndinakhululukidwa ndi Yesu, kupepesaku ndakulandira.
“Dziko lathu likuyenera kuchoka ku ndale zakale ndipo tizichita zinthu zofuna kupititsa patsogolo chitukuko ngati mmene amakambira mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pomwe amakamba zokhudza lamulo la malamulo,” watelo Msungama.
Pakadali pano mbali ziwirizi zagwilizana kuti mlanduwu ukambidwa kunja kwa khothi ndipo mbali ziwilizi zikuyenera kukanena kwa oweruza milandu a Justice William Msiska pazomwe angagwirizane zankhaniyi.
A Jeffrey anayankhula izi pomwe chipani chawo cha DPP chinali m’boma ndipo panthawiyi a Msungama omwe ndi a MCP anali mbali yotsutsa boma.