Ndithandidzeni ndalama ndimalizitse kujambula vidiyo, wapempha Martse

Advertisement

Katswiri oyimba nyimbo za chamba chotchedwa Hip hop mdziko muno, Martin Nkhata, yemwe amadziwika bwino ndi dzina lakuti Martse wapempha akufuna kwabwino kuti amuthandize ndi ndalama kuti iye amalizitse kujambula vidiyo ya nyimbo yake ku Blantyre.

Anthu omutsatila pa tsamba lake la mchedzo ati mkuluyi wawonetsa chamuna kubwela poyera kuti zinthu zamuvuta ndipo ngati alipo ena amuthandidze. Iwo ati anthu ambiri amakhala kuti akuvutika koma sabwela poyera kuwopa kuti anthu awaseka.

A Blessing Charlie poyankhapo pa nkhaniyi alemba kuti kupempha sikulakwa uthengawu ufike kwa anzake monga Fredokiss ndi Gwamba

Polankhula mwapadera ndi tsamba lino,  olemba nkhani za msagulutso Franco Mwachande Jnr wati Martse achepese kukonda kulemba chilichonse pa tsamba lake ndipo wapempha oyimbayu kuti amusiyile womuyang’anira wake kuti ndiye azilemba.

Mwachande anapitiliza kuti zolemba zili ndikuthekera kochosa chikoka chomwe munthu umakhala nacho kwa anthu okusatira poti pamakhala anthu ambiri omweso amakhala ndi maganizo osiyana siyana ndipo ndi bwino kukhala wa ulemu kwa onse .

Martse walandilapo mphoto zosiyana siyana ngati munthu oyimba bwino zedi , ndipo iye anakayimbapo ku mayiko a azungu. Zina mwa nyimbo zake zotchuka ndi monga Mwapindulanji, Mwano, Adidas ndi Tchwe! mwana tchwe.

Sitidakwanitse kulankhulana ndi oyimbayu mpaka nthawi yomwe timasindikidza nkhaniyi.

Advertisement