CDEDI yakonza zionetsero

Advertisement

Limodzi mwa mabungwe omenyera ufulu m’dziko muno la Centre for Democracy and Economic Development Initiatives (CDEDI) lati lipangitsa zionetsero sabata lamawa kaamba kakunyalanyaza kwa mtsogoleri wa dziko lino a Lazarus Chakwera pa nkhani zofunika.

Malingana ndi chikalata chomwe bungwe la CDEDI latulutsa, zionetselozi zichitika lachitatu pa 16 December ndipo ati zikayambira mumzinda wa Lilongwe komwe kalata yamadandaulo ikapelekedwe kwa mtsogoleri wa dziko lino kenaka ati zizachitikaso mmizinda ya Blantyre ndi Mzuzu.

Chikalatachi chomwe wasainira ndi mtsogoleri wa bungweli a Sylvester Namiwa chati bungwe la CDEDI laitanitsa zionetselozi kaamba koti masiku khumi ndi anayi (14) omwe anapelekedwa kwa a Chakwera, atha koma palibe chomwe chachitika.

Pa 23 November, CDEDI mogwirizana ndi ochita malonda ang’onoang’ono mmizinda ya Blantyre ndi Lilongwe anawuza a Chakwera kuti pasanathe masiku 14 ayankhe komaso kuthetsa ena mwa mavuto omwe bungweli linati akuchitika mdziko muno.

Mwazina, bungweli linauza mtsogoleri wa dziko linoyu kuti athamangitse anthu onse ammaiko ena omwe analowa dziko mophwanya malamulo ndipo akuchita malonda ang’onoang’ono zomwe ati zikupangitsa kuti a Malawi ambiri azikanika kuchita malonda ena.

CDEDI inauzaso a Chakwera kuti apange zotheka kuti chilungamo chioneke pa akuluakulu aboma ena omwe bungweli lati akukhudzidwa nawo pankhani ya kampani ya mafuta m’dziko muno ya NOCMA.

Bungweli lati ndizokhumudwitsa kuti mtsogoleri wa dziko linoyu wangokhala chete pa mavuto onse omwe akuchitika omwe anati ndikuphatikiza chimpwilikiti chomwe chikuchitika pandondomeko yogulitsa zipangizo zakumunda zotsika mtengo zomwe ati ngati siziyang’anidwa bwino, chaka cha mawa m’dziko muno mutha kukhala njala yadzaoneni.

“Masiku 14 omwe bungwe la CDEDI pamodzi ndimagulu aanthu ochita ma buzinezi ang’onoang’ono ku Lilongwe ndi Blantyre tinapeleka kuboma atha koma palibe kukamba kulikonse kuchokera kuboma zomwe zikusonyeza kunyalanyaza komaso kudelera kwa akuluakulu aboma.

“Ndiye kaamba kazimenezi Ife a CDEDI tikulengeza kuti tikuyamba kuchita zionetsero sabata lamawa pa 26 December zomwe ziyambile ku Lilongwe ndipo kenaka zifikiraso mmizinda ya Mzuzu ndi Blantyre. Chomwe tikufuna ndi mayankho kuchokera kwa a Chakwera pamadandaulo omwe tinawapatsa kale,” yatelo CDEDI.

Pakadali pano bungweli lati posachedwapa litulutsa tsatanetsatane wa mayendede patsiku la zionetserozi.

Advertisement