Wachiwiri kwa mtsogoleri wa chipani cha DPP mchigawo chakummwera, a Kondwani Nankhumwa, ati iwo akufuna pakhale kukambirana kuti kusamvana komwe kuli mu chipanimu kuthetsedwe.
A Nankhumwa amayankhula izi lamulungu pa Nyamithambo Arts Palace m’boma la Nsanje pomwe anapangitsa msonkhano omwe amakachezera anthu otsatira DPP mu mdelari.
Iwo anati zomwe zikuchitika mu mchipani cha DPP zakhalaso zikuchitika zipani zambiri m’dziko muno ndipo chipani chili chonse chimayenera kudutsa nyengo yomwe chipani chawo cha DPP chikudutsa.
A Nankhumwa anati chachikulu chomwe chikufunika kuti mikanganoyi ithe ndi chakuti akuluakulu a DPP akumane ndi iwo komaso anthu ena okhudzidwa pankhaniyi kuti akambirane za momwe angathetsere kusamvanaku.
Iwo anaonjezera kuti nthawi ino chipani chawochi chikuyenera kuunikira momwe chingapitile patsogolo ndicholinga choti chibweleleso m’boma pazisankho za chaka cha 2025.
“Zomwe zikuchitika mu mchipani cha DPP sizachilendo kwamunthu amene amatsata nkhani za ndale bwino bwino. Kunali AFORD, UDF, MCP onsewa anadutsa munyengo ngati imeneyiyi, nde zimenezi zikuchitika.
“Chachikulu chomwe chikuyenera kuchitika ndichoti akuluakulu akhale pansi ndimbali zonse zokhudzidwa ndipo zikatelo tili ndichikhulupiliro kuti zomwe zikuchitikazi zitha mosavuta ndipo 2025 DPP tibweleraso m’boma.” Watelo Nankhumwa.
A Nankhumwa anaonjezera kutiso mkofunika kwambiri kuti anthu akumidzi akhale ogwirizana ponena kuti akumudziwo ndiwo eni ake achipani cha DPP.
Chipani cha DPP posachedwapa chinalengeza kuti chachotsa a Nankhumwa komaso ena anayi ati kaamba kosatsata ena mwa malamulo achipanichi koma akuluakuluwa anakatenga chiletso kuletsa kuti iwo asachotsedwe mchipanimu.
Pakadali pano mneneri wa DPP a Brown Mpinganjira ati chipanchi chiyankhulabe pazomwe ayankhula a Nankhumwa zi.