Madalaiva omwe sanatsitse mtengo azimangidwa – yatero MOAM

Advertisement

Bungwe la eni maminibasi m’dziko muno la Minibus Owners Association of Malawi (MOAM) lati oyendetsa ma minibasi onse omwe sanatsitsebe mitengo yawo akuyenera kumangidwa.

Wayankhula izi mlembi wamkulu wa bungweli a Felix Mbonekera omwe anati ndizokhumudwitsa kuti oyendetsa maminibasi ambiri akupitilirabe kulipilitsa anthu mitengo yokwera ngakhale kuti mafuta atsitsidwa mtengo kawiri kose.

A Mbonekera anati akuluakulu a MOAM pa 8 mwezi uno anakhala pansi ndikugwirizana kuti mitengo yokwelera maminibasi itsike ndi K14 pa K100 iliyose potsatira kutsika mtengo kwa mafuta zomwe ndikaamba ka nthenda ya COVID-19.

Iwo ati ndizokhumudwitsa kuti anthu akupitilirabe kulipira mitengo yokwera kwambiri ndipo ati izi ndikuphwanya malamulo a bungwe lawo ndipo alamula apolisi kuti ayambe kumanga madalaivala onse omwe akugwiritsabe ntchito mitengo yokwerayi.

“Ife a Minibus Association of Malawi tinakhala pansi ndikugwirizana kuti mitengo mmene timatchajira kale itsike ndi K14 pa K100 iliyose izi zimatanthauza kuti oyendetsa minibus aliyese agwiritse ntchito mtengo umenewo.

“Panali pa 8 May pomwe tinakumana ndikugwirizana izi potsatira kutsitsidwa mtengo kwa mafuta kawiri ndipo tikunena kuti amene sakutsatira izi mkwabwino kuti apolisi awagwire ndithu,” anatero Mbonekera.

Iwo anatiso anaikaso ndondomeko yoti shoveli aliyese ayike mtengo omwe akugwiritsa ntchito pa galasi lakutsogolo ndicholinga choti okwera adziona mitengoyo asanakwere galimotoyo kuti aziona kuti komwe akupitako ndi mtengowo ndiogwirizana.

A Mbonekera anatiso izi zimayenera kuchitika mummadera onse mdziko muno koma ati vuto ndiloti oyendetsa minibus ena amangopanga zoti ziwakomele iwowo basi osafuna kusangalatsa makasitomala awo zomwe anati sizabwino.

Mkuluyu anaonjezeraso kuti nkhaniyi apolisi a pansewu akuidziwa ndipo anawauza kuti minibus iliyose yomwe oyendetsa wake sanaike mitengo pa galasi ndekuti akubera anthu ndipo azimupatsa chilango.H

Advertisement