Abambo awiri apezeka akugulitsa chiberekero cha mayi

Advertisement

Abambo awiri ku Ntchisi ali mu chitokosi atapezeka akugulitsa chiberekero cha munthu pa nsika wa Ng’ombe m’bomalo.

Mneneri wa a polisi ku Ntchisi a Richard Mwakayoka Kaponda anena kuti anamanga abambo awiriwa patamveka mphekesela kuti abambowo amagulitsa chiberekero cha munthu pa nsika wa N’gombe.

“Patamveka mphekesela zoti abambo wena akugulitsa chiberekero pa nsika wa Ng’ombe, ife a polisi tinathamangilako kukafufuza za nkhaniyi. Uko tinapeza abambowa akugulitsa chiberekero cha munthu. Izi zinapangitsa kuti abambowa amangidwe.

“Titawafutsitsitsa azibambowa anaulula kuti iwowo akusakasaka nsika wa chiberekero ndipo anati akugulitsa pa mtengo was K3 miliyoni,” anatelo a Kaponda.

A polisi ku Ntchitsi adakafufuzabe kuti apeze mayi yemwe wachotsedwa chiberekeroyo.

Omangidwawo, bambo Matias Joseph a zaka 20 ndi bambo Masiwin Joseph a zaka 30 amachokela m’mudzi mwa M’dzeranji kwa Mfumu yaikulu Malenga ku Ntchisi komweko.

Advertisement