A polisi ku Mulanje amanga bambo George Naphazi a zaka 48 powaganizira kuti akhala akuba nthambo zamagetsi ndi katundu osiyanasiyana.
Bamboyu wamangidwa anthu akufuna kwabwino atakamuneneza kuti wakhala akuba nthambo za magetsi komanso katundu osiyanasiyana.
Mneneli wa a polisi ku Mulanje, a Gresham Ngwira ati atatsinidwa khutu ndi anthu akufuna kwabwinowa kuti bamboo Naphazi akumaba katundu wa wanthu, apolisi sananyozele koma kupita kwa bambowa kukapanga chipikisheni.
“Anthu akufuna kwabwino atatiziwitsa zoti bambo Naphazi akhala akuba katundu osiyanasiyana ife sitinanyozele koma kupita kunyumba kwao kukapanga chipikisheni.
“kumeneko, tinapezako katundu obedwa osiyanasiyana monga ma kompyuta awiri, batile lagalimoto, maphone ndi zina zambiri,” anatelo a Ngwila.
Bambowa amachokela m’muzi mwa James, Kwa mfumu yaikulu Mabuka m’boma la Mulanje.