M’busa anjatwa, akuti Mulungu anamuuza kuti agwililire

Advertisement
Malawi

M’busa wina m’boma la Phalombe wa njatwa ndipo wagamulidwa kukaseweza jere zaka khumi ndi mphambu imodzi (11) kaamba kopezeka olakwa pamlandu ogwililira mwana wazaka khumi ndi mphambu zitatu (13).

Malingana ndi mneneri wa apolisi m’bomali a Innocent Moses, m’busa onyengayu wadziwika kuti ndi John Mkumbira yemwe ali ndi zaka makumi atatu ndi mphambu ziwiri (32) zakubadwa.

Mneneri wa apolisiyu wati m’busayu kwakanthawi wakhala akumamutenga mtsikanayu ku phiri la Michesi m’boma lomweli komwe akuti amakapemphera naye.

Malipoti a apolisi m’bomali asonyeza kuti mkuluyu wakhala akumugwililira namwaliyu kochulukirapo kufikira pomwe wamangidwa mkatikati mwa mwezi wa Disembala.

Apolisi ati nkhaniyi inadziwika makolo amwanayo atamupanikiza ndi mafuso pazizindikilo zomwe zimawakaikisa ndipo nkhaniyi akuluakulu anaitengera kwa apolisi omwe sanachedwa koma kumanga mkuluyu.

Atafusidwa cholinga chomwe amapangira zinthu zochitisa manyazizi, m’busa Mkumbira anati Mulungu ndi amene anamuuza kuti agone ndimwanayo ndicholinga choti mwanayo azikula muuzimu.

Apa bwalo lamilandu la Phalombe first grade magistrate linagamula mkuluyu kuti akakhale kundende ndikugwira ntchito ya kalavula gaga kwazaka 11 kuti likhale phuzilo kwa azibambo enaso amalingaliro ngati awa.

Munthu wa Mulunguyu amachokera mmudzi wa Mbodi mdera mfumu yaikulu Nkhumba m’boma lomweli la Phalombe.

Advertisement

One Comment

  1. Azibusa ambiri alibe maitanidwe a Mulungu. Alowa ntchitoyi kungofuna kudetsa dzina la azibusa okhala ndi maitanidwe. Ayi ntchito za manja ake zimuchitire umboni. Koma dziwani ichi alipo ambiri anchitidwe woterewu koma sanagwidwe. Samalani la 40 likwana

Comments are closed.