Ntchito 1 miliyoni pa chaka? Haha ndi bodza la nkhukuniza – Mutharika

Advertisement
Peter Mutharika

Wandisokosela n’kulinga utamva, ndipo chulukechuluke ngwa njuchi yomwe umanena iwe ndi yomwe yakuluma.

Peter Mutharika
Mutharika: Chilima wabodza

Mtsogoleri wa dziko lino a Peter Mutharika wati zomwe akunena wachiwiri wawo a Saulos Chilima zoti pasanathe chaka azakhala atapanga ntchito 1 miliyoni ndi zabodza.

Malinga ndi uthenga ofuna kuutsa mudyo a Malawi kuti amvele ndi kuonela pologalamu imene a MBC akhale akucheza ndi a Mutharika, a Mutharika akunena kuti ndi nthabwala zoti munthu atha kukhazikitsa ntchito 1 miliyoni ku Malawi kuno.

A Chilima anasiyana ndi a Mutharika ndi kukayambitsa chipani chawo atalephera kuchotsa a Mutharika pa udindo otsogolera chipani cha DPP.
Pokhazikitsa chipani chawo, a Chilima anauza a Malawi kuti akawasankha iwo azapanga ntchito 1 miliyoni kuti a Malawi osowa ntchito apeze pogwila mu miyezi isanu ndi umodzi yokha.

Advertisement

10 Comments

 1. Hahaha 1 million Jobs in 5 month time!! Achilima bodza samatero amalawi pano samava zopusazo ”!!

 2. Hahaha 1 million Jobs'””!! Achilima bodza samatero amalawi pano samava zopusazo ”!!

 3. Pajatu wapakaliyala samaimba belu monga anatiuzila malemu Bingu so it was not easy for Chilima to create 1 million jobs while by the kaliyala so tanamizidwa m’buyomu nde tionenso izizi but the man is confident kuti zontheka ngati iwe ukuyesa ndinthabwala mnyamata wati amanga ma standi mukhale kumeneko mudzionerela baby akupotokola chiongolero towards creating 1 million jobs inuyodi kukayika kwake kumeneku tinabetsa mtsogoleli sayenera kukhala wokayika otelo amafunika kukhala owonelera osati kutsogolera.

 4. Kd inu a DPP osapanga zanu bwanji ? Musiyeni apange zomwe akudziwa,osati mudzimulondalonda.

 5. Achilima zimene akukamba Ku misonkhano zonse ndi nkhamba kamwa chabe ,sizingatheke oro mpangono pomwe says:

  Achilima zones zomwe akukamba kuminsonkhano yao ndiza bodza ,created ajo in one yr 1 million ,even maiko olemelao sizinanthekepo ndiye akaziyambe iye akazitenga kuti ntchito zo

 6. kodi ntchito 1 million amadikira kuti achoke mboma, Achilima musamawatenge ngati amalawi ndi osadzindikira, we are not stupid we know that you , kaliat and others you are just greedy people

 7. Chilima the true hope of Malawians ndipo usauzile mayeso chilima apumbwa angabele go boy go

 8. koma bwana pulezidenti mukundidandaulitsa zedi. ozchitika zanu zikuonetsa kuti mutu wanu siukugwira. mukutay nthawi ndikuyankha zopanda phindu m’malo moyankha nkhani ngati.
  1, zokweza magetsi
  2. 145 million kwacha
  3. xul kumugwera mwana mpakana kufa
  4. nkhani zoti akulu anu anapha chasowa
  5. kuzimazima kwa magetsi

  pali zambiri zoti muyankhule zomwe zingaonetse kuti ndinu pulezidenti koma mungolubwalubwa

Comments are closed.