Lero kulibe mwambi: wamkulu wa Katolika ajiya ya Chilima

Saulos Chilima Catholic Church

Kukanakhala kuti pachiweru kunali mwambi, kaya a Chilima akanagwilitsa uti kaya? Koma pomaliza kulankhulapo pa mwambo odzodza ansembe a chikatolika pa Limbe Cathedral a Chilima anatsindika kuti kunalibe mwambi.

Saulos Chilima Catholic Church
“Tikujiya ya inu”

Koma ngakhale panalibe mwambi ochoka kwa a Chilima, sikuti akulu a mpingo wa Katolika anaisiya chabe ndeu yomwe a Chilima akuyesa kulikhana ndi a Peter Mutharika.

A Luke Msusa amene ndi wamkulu wa Katolika mdziko muno akudzudzulidwa atapenekela kuti iwo ali pambuyo pa a Saulos Chilima.

Pamene amayankhula pa mwambo omwewo umene a Chilima anakanika kuponya ka mwambi, a Msusa anati anthu ayenela kusankha atsogoleri a masomphenya, osintha zinthu ndi oopa Mulungu.

Iwo anaonjezelapo kuti ngati anthuwo ali ochoka mu mpingo omwewo, ndiye anthu basi anyonyomale kumbuyo kwawo. Izi anthu ati amanena pochemelera a Chilima amene akhala akuthyakula mikuluwiko ya ndale pa guwa la mpingo wa Katolika.

Koma anthu ena adzudzula a Msusa kuti iwo ngati mkulu wa mpingo sali oyenela kutelo.

Advertisement

6 Comments

  1. Iwe wag usakhale ngati wabadwadzulo kusintha kwake kuti? Analipo anKati asintha zithu ndiye zinasintha?uyuso angofuna zake zizayele basi

  2. Let chilima rule the country i see thing changing in other side

  3. Everyone has his choice even priests. Ndani opusa akusangalala nazo zomwe zikuchitika piano.

  4. Everyone has his choice even priests. Ndani opusa akusangalala nazo zomwe zikuchitika piano.

  5. Msusa doesnt deserve to be slamed, ndani sakufuna zinthu zitasintha?

  6. Kodi Professor Peter Mutharika ndi wa Mpingo uti? Koma 1992 ma Bishop said the same thing, ta people need to be enlightened on such issues. Mutharika has monopolised MBC, it’s just a platform for him & him alone so what do you expect from other people? If the Bishops feel that that Chilima is the one let them tell the people but it doesn’t mean that everybody will vote for him. The point Bishops put is the one which is very important, that anthu asankhe Atsogoleri a masomphenya. If Chilima fits in that category let him be the one.

Comments are closed.