Zida zija anasula a Mutharika kuti anyenye a Chilima ndi owatsatila tsopano zilibe ntchito. Kutukwana konse amachita Mayi Kaliati nako kulibe fungo. Tsogolo silikuoneka bwinobwino. A Chilima ati afotokoza bwino lino.
Atakola chidwi cha a Malawi dzulo pa tsogolo lawo la ndale, wachiwiri kwa Mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima akanika kufotokoza bwinobwino tsogolo lawo pa ndale.
A Chilima dzulo anaitanitsa atolankhani ati kuti akathilepo ndemanga pa zochitika za ndale mu dziko muno. Izi zinabwela pamene anthu ena mu chipani cha DPP amamema a Chilima kuti akapikisane ndi a Mutharika.
Koma polankhula pa msonkhano wa atolankhani umene anachititsawo, a Chilima analengeza kuti iwo sakapikisana nawo ku msonkhano waukulu wa DPP pa udindo ulionse.
Iwo anati anthu amene amaima pachulu kuwapempha kuti iwo aimile, sikuti anachita chotumidwa.
A Chilima anadandaulanso kuti dziko la Malawi likusokonekela ndi anthu adyera, a katangale kudzanso a tsankho.
Pa za tsogolo lawo pa ndale, a Chilima adanena kuti alengezabe.
Koma iwo anaulula kuti ayambapo ndondomeko yosamuka mu chipani cholamula cha DPP.
Zokamba za a Chilima zikuoneka zasokoneza a Malawi owakonda ndi omwe samawakonda maka mu chipani cha DPP.