TNM 4G Lite Flash

By December 5, 2017

…chipani cha DPP chikhumudwa nawo

Wachiwili kwa Mtsogoleri wa dziko lino a Saulos Chilima anauza a Malawi kuti apite ku zionetselo pa 13 December chaka chino.

A Chilima ananena izi mu mpingo wa katolika ku Lilongwe. A mpingo wa katolika anayika pa zolengeza zawo nkhani yopempha ma membala a mpingo wawo kupita ku mseu kukaonetsa mkwiyo wawo ati poti a boma akuchedwa kukamba nkhani ya malamulo a kavotedwe.

Saulos Chilima

Chilima: Pa 13 December, tiyeni mukamatche.

Pa mpingo wa St Patricks umene a Chilima ndi membala, iwo ndiwo anapatsidwa zolengeza kuti anene.

Atafika pamene mpingowo umadziwitsa ma membala awo zopita kumseu, iwo analengeza.

“Pa 13 December, tiyeni mukamatche. Muzavale yunifolomu ya Tchalitchi,” iwo anatelo.

Anthu ena otsatila chipani cholamula cha DPP ati akhumudwa ndi khalidwe la a Chilima amene amamema anthu kugalukila boma lawo lomwe.

“Izi si zoona anachita a Chilima, mesa iwo ndi gawo limodzi la boma? Tsopano iwo sakanatha kupempha kuti asanene zolengeza? Apa sanaganize bwino,” anatelo wina otsatila DPP.
2 Comments

  1. MBWFC says:

    chilima sanalakwitse,nanga ukanakhala uthenga woipitsa chipani cha MCP mukanati alakwitsaso kupanga zolengeza??? mmmmmmmmmmmmm asiyeni achilima

  2. Kanyimbi says:

    Chilima was at church as a catholic member and not a government delegate, He had two things to choose, God or DPP. If you were in that situation what could you have done? Leaving God to serve a political party?

Leave a Comment

%d bloggers like this: