Makoswe athamangitsa Pulezidenti mu ofesi

Buhari

Anthu ena akudabwa kuti anali aakulu ngati n’gombe mwina kapena ochepa koma msinkhu wa mphaka kapena mwana wa khanda.

Mtsogoleri wa dziko la Nigeria a Muhammadu Buhari alengeza kuti sazipita ku ofesi yawo ati chifukwa kuli makoswe amene aononga ofesiyo.

Buhari
Muhammadu Buhari: Asiya kupita ku ofesi kamba ka makoswe.

A Buhari amene afika ku Nigeria kumapeto a sabata yatha kuchokela ku dziko la Mangalande kumene anali kuchipatala kwa miyezi yoposa itatu anauza mtundu wa anthu ku Nigeria kuti iwo akhala akugwilila ntchito kunyumba kwawo. A Buhari ananena izi kudzela kwa othandizila.

‘Chachitika ndi chakuti pa nthawi imene ofesi yawo sinali kugwila ntchito, makoswe anasandutsa mphala yawo ndiye aonongamo,’ anatelo owathandizila a Bushiri kuuza mtundu wa anthu a ku Nigeria.

Koma ngakhale alengeza zotele, sikuti anthu akhulupilila kuti a Buhari akuthawa makoswe. Anthu ena mu dzikomo akuganiza kuti a Buhari sanachile zenizeni ndipo akufuna azigonabe.

A Buhari akhala akudwala kuyambila chaka chatha ndipo chaka chino nthawi yawo yochuluka yathela ku chipatala ku Mangalande.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

Advertisement

2 Comments

Comments are closed.