Ogwila ntchito mmboma muvale zilimbe, ati malipilo anu achedwa

Advertisement
Hunger Malawi

Anthu onse ogwila ntchito mmboma ayembekezela kukokana ndi ma landilodi mwezi uno chifukwa boma lalengeza kuti malipilo awo alandila pa 45.

Malinga ndi chikalata chimene chalembedwa ndi a unduna wa zachuma ndipo chasayinilidwa ndi a Ben Botolo amene ndi mlembi mu undunawu, iwo ati anthu ogwila ntchito mu boma mwezi uno avale zilimba.

Civil Servants
Botolo: Malipilo achedwa.

Chikalatacho chati izi zachitika chifukwa ma unduna ena anachedwa kupeleka zikalata zina zimene zimagwilitsidwa ntchito kulipilila malipilo a anthu ogwila mu boma.

A unduna wa zachuma ati malinga ndi mwambo, mapepala a  anthu oyenela kulandila malipiro awo amayenela kupelekedwa ku unduna wa zachuma pa 16 pa mwezi ulionse koma ati ulendo uno ma unduna ena anachedwetsa ndiye izi nazo zichedwetsa malipilo.

Iwo ati anthu amene ali pa chiopsezo cholandila pa 45 ndi ogwila ntchito ku nyumba ya malamulo, a Polisi, a ku unduna wa za migodi kudzanso anthu onse ogwila mu ma khonsolo kupatulapo Likoma basi chifukwa iwo anapeleka mu nthawi yake.

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

 

Advertisement