Chiwamba ayipidwa ndi malipiro a pa Malawi

124

Mlakatuli Robert Chiwamba mu ndakatulo yake yomwe watulutsa kumene wadandaula ndi malipiliro omwe olemba ntchito akupatsa anthu a ntchito.

Mu ndakatuloyi yomwe mutu wake ndi “Malipiro Pa Malawi Pano”, Chiwamba wanena kuti ndalama zimene amalawi akulandira zitha kumawaonetsa ngati anthu osadziwa kugwiritsa bwino ntchito ndalama.

Malawi poets

Chiwamba: wayipidwa ndi malipiro pa Malawi.

“Malipiro akupelekedwa pa Malawi panotu ndi otukwanitsa. Malipiro akupelekedwa ntaunimutu ngoliritsa. Ndithu malipiro akupelekedwa mdziko munotu ndi okuyambitsa ndeu,” watero Chiwamba mu ndakatuloyi.

Malingana ndi Chiwamba, malipiro a pa Malawi pano atha kuonetsa ngati munthu ndi odzikonda komanso osasamala za anthu ena.

“Mwezi wathatu a Bae mutitumizileko mayunitsi. Umangotsonya pansi pamtima umvekere utsiru wakowo. Poyang’ana zomwe ukupatsidwa pamwezi ngati ntchito sukugwila,” ndakatuloyi yatero.

Mlakatuluyi wanena kuti anthu amene ali pantchito mdziko lino amakhala akugwa mngongole zankhaninkhani chifukwa chakuchepa kwa malipiro awo.

Mu ndakatuloyi, Chiwamba wati anthu ena ngakhale kumwamba kukawanikanika chifukwa chokhala ndi ngongole polingalira kuti munthu wokongola ndalama kwambiri amafunika azikhala wodziwa bodza lothawira a ngongole.

“Nokha mukudziwa kuti ngongole ndi bodza ndikhethekhethe choncho umfumu wa achina Eliyawo ungakuone,” watero Chiwamba mukulakatula kwake.

Chiwamba walangiza anthu amene amalemba anthu ntchito kuti aganizile anthu awo antchito ndiponso ngati ndikotheka athe kuwaonjezera kuti adzikwaniritsa kugula zofuna zawo.

Mlakatuliyu wadandaulira achinyamata omwe amakapanga maphunziro a pamwammba koma kumalandira ndalama zongokwana kugulira matumba awiri a feteleza .

“Achinyamata kumaliza maphunziro a zaukachenjede ndi chiyembekezo chamapiliro a phwamwamwa koma mphuno salota kumapatsidwa ndalama zosakwanira matumba awiri a fertilizer okulitsa. Munthu kulusa kufuna kudzipha koma ukabweza ngongole zako zonse ndalama yotsalayo osakwanira kugula tameki,” watero Chiwamba mu ndakatuloyi.

Chiwamba watulutsa ndakatuloyi komanso ina yomwe mutu wake ndi “Dziko lapansi ndi lokondera,” ngati mbali imodzi yosangalala kuti wakwanitsa zaka zisanu ndi chimodzi akupanga za ulakatuli.

Ndakatulozi zikupezeka pa sapitwapoetry.com

 

 

 

Share.

124 Comments

 1. Na Ku Ministry Of LabourPalibe Chomwe Amapanga Nkhani Ndi Kukhutitsa Mimba Zawo Basi Anthu Akuzunzika M’ma Company Malipiro Ochepa Kuchitilidwa Nkhaza Pamene Boma Lili Phe Kadziko Kakang’onong’no Koma Umphawi Wadzaoneni Ma Mp Athu Sakutithandiza.

 2. The one who has peanuts will try to share them with the other, and is a sacrifice, must be thanked. Such people are called heroes. Tsopano inu Bambo Chiwamba, don’t forget muli ku Malawi osati ku America, ndipo salary imamvesa chisoni.

 3. Ali Ndi Luso Lolankhula Mwa Luso Pa Mau Omwe Wawasakaniza Koma Izi Si Ndakatulo Mwa Malamulo Ngati Ndizomwe Amanphuzira Ku Chanco Ndiye Mwina Tifunse Anyama Likiti Mwina Ku Malawiko Malamulo A Ulakatuli Munasintha, Tiwuzeni Zowona A Kazako

 4. Vutotu so olemba anthu ntchito koma malamulo athu ndomwe ali opusa kwambiri chifukwa sakakamiza olemba anthu ntchito kupereka malipiro ambiri. Ndipamene olemba anthu ntchitowo amapezerapo Mwai.

 5. in a democratic country where citizens are afraid to voice out for their rights. Teach them to know their rights. mmalawi amafuna ena azimumenyera nkhondo koma akapeza ulemelero kunyozanso

 6. Achiwamba muxiyenda mosamala sikuti andalewa angamakuoneni bwino komaso kumawerrengako za mzanu anachitidwapo chipongwe uja chasowa ndiye samalani.ife ulakatuli wanu umatisangalasa.

 7. Zoona zokha-zokha koma kuona kwaine vuto ndi boma komanso eni ake amalawi timapangilana nsanje tokha-tokha chisanzo kuno afuna kupanga damu musinje wa south rukulu ndiye azungu ankafuna patsiku munthu azilandila k3,000 koma amalawi akuti ayi zimenezo kuno kulibe anthu azilandila k1,500.Chonsecho amalawi omwe alikutsogolo akulandila k6,000 patsiku nsanje tokha-tokha amalawi.

 8. Vuto ndi unduna wa zantchito sugwira ntchito yake koma kulandira ziphuphu kwa amwenye. Komanso or atangouthetsa unduna umenewu because akungo kudya ndalama zosagwilira ntchito.

 9. Komanso vuto ndi boma,particularly Ministry of Labour alibe nthawi yowalankhulira anthu ogwira ntchito mu private sector kaya ma company,amwene,mma china,mma NGOs.

 10. amwenye anthu okuda. ngakhale azungu malipilo ndiochepa basi just because of our government thats why many people they left malawi suffering other countries

 11. Malawi sadzatheka axanthu apa Zambia ponpa malipiro ndi abwino km kuno timachenje teniteni chikhalireni tikumalowa shop imodxi ndi achumawo

 12. Komatu munthu walankhula zoona kungoti chilungamo ndichowawa. Munthu kumalandila 40,000 kwacha rent,school fees,kumunda,transport, makolo,kudya daily mmmm mabvuto pamalawi

 13. Zoona zokhazokha kotelo kuti antchitowo akamaba asamanenekuti ndioipa koma kutengela ndi salary yomwe amalandila akungoyenera kumaba

 14. Whenever an issue of malipiro comes up mma company mu, their reply is “ndi boma lanu”. Meaning salary structures of Malawi government through the department or ministry of labour are very poor. Infact, i think those in the decision making are still using colonial salary scales. And most business people who are Malawians are very greedy to pay better salaries to their own of which they even discourage investors when they come to pay good salaries, they say kuno sititero. I don’t understand, at the end of the day, most Malawians are just working hand to mouth

 15. Amwenye akupanga phindu lochuluka km ogwira ntchito awo malipiro nd omvesa chisoni akalembana amwenye okha okha nde amakhutulirana dzi makobidi… Tiye nao m’bale wanga #Chiwamba

%d bloggers like this: