Palibe kusweka motchipa achinyamata: Midori ayichotsa pa msika

Advertisement
Midori

Tiyeni tichepetse zoyaka mammawa izi ndi kuyamba kulimbikila tsopano chifukwa mowa otchipa uja auchotsa pa msika.

Anthu atadandaula za kapezekedwe ka mowa mu ma botolo a pulasitiki ndi mu masacheti, zikuoneka zamveka tsopano.

Midori
Mowa onga uwu akuwuchosa pa msika.

Kampani zopanga mowa umene umapezeka mu ma botolo a pulasitiki tsopano ati zayitanitsa mowa wawo atamvana ndi bungwe la Malawi Bureau of Standards (MBS) kuti atelo.

Malinga ndi malipoti otsindikizidwa mu nyuzipepala, kampani zopanga mowa zinakhala pansi ndipo mwa zina agwilizana kuti mowa onse wa mu pulasitiki usiye kupangidwa.

Padakali pano, agwilizana kuti mowa umene uli kale pa msika ukabwenzedwe ndipo ogulitsawo akalandilapo zawo.

Wina mwa mowa umene waitanitsidwa ndi wa Super Midori ndi Midori umene unakondoweza achinyamata ambiri mu makwalala umu.

Achina Boss Whisky, Flames Rum, Zero Gin, Blank Ponda Rum ndi Tyson Cane nawo awaitanitsa.

Shooter Premium, Vodka, Empire cane spirit ndi Chilwa manufactured by Chilwa kuphatikizapo Three Kings ndi Rio Gin nazo zaletsedwa pa msika.