Kumseu kwavuta: wa minibus wina amulipilitsa K480,000 poyenda opanda chitupa ndi kunyamula ma 4 – 4

Advertisement

Chaka chino ndiye zonyengelera kulibe. Apolisi a pamseu akwiya ndipo nonse opitiliza chibwana samalani chifukwa mutha kupeza mavuto.

Mkulu wina oyendetsa minibus wayetsa malodza atagamulidwa kuti alipile ndalama zokwana K480,000 atapezeka kuti amayenda opanda license komanso galimoto yake idalibe zitupa (CoF).

Malinga ndi malipoti, Apolisi adagwila Bambo Julius Pofera mu mzinda wa Lilongwe atawapeza kuti iwo amayendetsa minibus alibe license.

Apolisi ati kuphatikiza apo, adapeza kuti minibus imene amayendetsayo idapezeka kuti inalibe chikalata choiyeneleza kuyenda pamseu (CoF).

Pamwamba pakenso, iwo adanyamula anthu moonjeza. Ati atagwila minibus inali itapakila anthu 20 zomwe ndi zosaloledwa pamseu.

A Pofera atagwidwa anatengeledwa ku bwalo la Milandu mu mzinda omwewo wa Lilongwe kumene anakapezeka olakwa.

Bambo Pofera anapempha bwalo kuti liwachitile chifundo chifukwa kanali koyamba kulakwa komanso ali ndi banja loti alisamale.

Koma Apolisi anapempha bwalo kuti likanthe Bambo Pofera ndi chilango chokhwima kamba koti ngozi zikuchuluka ndipo iwo akufuna anthu atengelepo phunziro.

Poweluza a bwalo anagamula Bambo Pofera kuti alipile K480,000 kapena akagwile wa kalavula gaga kwa miyezi makumi awiri ndi umodzi (21).

Advertisement

203 Comments

  1. This is not fair mukuyiyamwa ng’ombe yoondakale why u don’t arrest Chaponda Malawi walero obera anthu osauka olemera akapalamula salandila chilango chilichonse.One day God will judge us remember.

  2. Ndiye Malawi Wanga Ameneyo! Dzikoli Akuliva Bwino Ndi Alendo Koma Mnyasa Ataaaa! Mitsokho Mutidule Mwankhaza Koma Iiiii! Basibe Ndife Amalawi Koma Tisikondana Coz Nyimbo Ija Ya Mtundu Wa Fuko Lathu Muli Fundo Zomanga Malawi Osati Nkhazazi Ayi

  3. umbava wa apholisi ,kuponderezana uku &with zis situation sitingalemere,mmalo moti azikalimbana ndi umbanda ndi umbava akungothamangira pamsewu nkumatichedwetsa maulendo opita kumaliro.Angopita ndikukayitanira ma min-bus ngati ali moneyhungry.

  4. Nanga minbus ikudusa pa roadblockyi bwanji sakuigwila chonsecho anthu ali 4~4 pampando uyu ndie ndalama phwii.kuba basi nkhani ndi licence kapena zina?

  5. a police sakulakwa ndi mawu anayankhulidwa chikuvuta ndi chani kwa sunga mawuwo amaminibus musamapange zinthu ndi cholinga chofuna kuwaona ena Ngati zitsilu kapena opusa kumakhala seriously ndi ntchito yanu osati ife tingamakuloweleni kumaika ndemanga zokubakilani ndinu Mbuzi kumava mulungu anakuikani makutu mbali yakumanja ndi mbali yaku manzele kuti muzisowa ponamizila kuti simunave nde analengaso mphepo kuti wina akalankhula mawu aziyenda ndi mphepo IJA azikalowa nmakutu mwanumo ntchito ya bwino a police osasekelela zompusa nmanja mwanu

  6. Zalowano kubelana, the need for money is too much in this government, amakhwimitsa malamulo okhaokha omwe akukhuzana ndi za ndlama basi. Anthu akubeledwa daily koma palibe chomwe akupanga

  7. No certificate of fitness, No driving license, komanso 4 4. minibus oxcart? Kumeneku ndiye kutengera malamulo mmanja. Chilango chachepa ichi.

  8. Good
    Apolisi apitipize ndithu zimenezo
    It’s Fair cos amakhala atanyamula anthu kodi akapanga ngozi anthu afe zimasangalatsa?

  9. zinthuzi zangokhala zovuta, kulipilisidwa 4,8000 00, mm mzovuta ndiye dziko lapansi m’ene zikhalila mu ulemelelo zimenezo zolangana pansi panozi kwa mwini mfumuyo kulibe, mkomwe pa tsikulo tikazafika ngati tichita bwino m’oyo uno mkukaonanana mkumati abwenzi taonani takumana kuno titazunzana kwa nthawi yaitaali m’oyo wa Ku dziko, chosangalasa mkuwiyobsuzakhalako, mau akunena momveka kuti, zaakale sizizakumbukilikanso. mukuziwa inu anthufe tizapulumuka chifukwa cha, chisoni. bwanji tsopano tifewese mtima yathu tisaumile anthu mtima izakhalapo nthawi mkumamva kuti iiiiinuuu inu munayenela kupita Ku gahena, koma, komatu chifukwa choti unmukhululukila uyu, sunalandile chinyengo, sunakamponye mundende chifukwa cha nkhani za pa nseu, lowa m’chikondwelelo cha state nanga, lomwe kuzakhale kuimba mkukondwa, mwalankhulidwatu iiinu, sinthani. mulungu, akudaliseni nonse.

  10. Nanga a njingaza moto akumakwela antju four njinga Imozi Komaso opanda licence insulance Komaso helmet AKumayenda Nthawi zonse ndi liwilo lalikulu NGati Ali part MPikisano Kuti opambana Alandila MPoto awapanga Chani nawoso agwidwe Alipilisiswe chindapusa chambili

  11. Amalawi kumaivesesa nkhani .munthuyu wanali driver koma chinali chigawanga chosasamala moyo wanga anthu ,chifukwa wamayendesa galimoti alibeso chiphaso choyendesela galimoto kuli kupwanya malamulo koyamba komaso kusasamala miyoyo ya anthu.komaso nkupakilaso molakwila malamulo.ndiye muziti a police ngolakwa.?aaaaa inu!!! what abt wanakataya anthuwo. ? wamayendeselanji galimoto wopanda chiphaso chapamusewu.?

  12. Bola chilungamo chikhalepo mwayamba ndimoto inu apolice mapeto ake muyambe kukanilana.kma zikuoneka ngat mukupanga zosiyana,akumulanje k180,000,nanga inu mpaka k480,000.nanga kuiwala chitupa mpaka kuonjezela k300,000 its too much.

  13. Ndalamayonso Yachepa.Akanawaonjezera.AMinibus Amakhala Ngati Saopa Munthu Ngakhalenso Lamulo.Akutikweza Ngati Matumba Osati Anthu.Ndalamayo Yachepa.

  14. Out of his ignorance, he has to face it. For they loved the drivers they announced their beloved laws, and those who are to follow the law, they will enjoy their business..

    Lesson to drivers,, ignoring the law is very expensive. Just abide to the law or rules you will be happy people,

    Big up law enforcers,, let us learn to teach how to teach those who are required to be taught..

  15. Komanso nkumati pamene pali a policepo mpanseu or pa tchile.
    Akupanga zobisalilana bwanji?
    Wa police or speed trap amafunika kukhala poyela osati kumabisala ngati ndakuba

  16. Nanga lincese ingayendese galimoto opanda munthu? Nanga okuba afuti mukulephera kuwagwira bwanji? Nanga akuba mankhwala mudzipatalawa… Milandu ya ziii ndalama phwii!

  17. Koma ma Driver enawa amakhala opanda nzeru, zoona iyeyo kunyamuka kumaenda pansewu opanda Licence? Nanga umbon oti ndi Driver ndi uti? Nanga pakachitika ngoz, adzadziwika kut Driver ndi uti? Amuchita bwino, kip it up. Ma 4-4 musiyeso

  18. Dandaulo langa ndiloti ndalamayo yachuluka and munthuyo aliso ndi mavuto so plz think b4 you judge someone u too u will be judged.

    1. Allan! Check a point, last few weeks ago a police ena ku Thyolo anaba ndalama za anthu awiri for nothing reason and today look now what happens in Lilongwe, u think it’s fair pa zomwe a police akuwachitila anthu? ?

    2. A police sakugwira ntchito yawo motsata ma lamulo coz wa mini bus aliyense akamadutsa pa road block amanyema kenakake akuti ka Fanta for what? ?Corruption ndi yomwe yatenga mbali yayikulu pa Malawi, kupondelezana kutelo palibe yemwe angatukuke.

    3. COF mbola, Licence mbola kupacira 4 pampando mbola olo munthu omvera cisoni iyeyu angayambire pati? Ndipo nkhani nd corruption sizikugwirizana amucita bwino mwinafi ena angatengerepo phunziro

    4. Umbuli siwabwino enanu mukupanga comment nkhani zosiyana ndiyomwe yili yapa.Choti mudziwe amagamula siapolice koma a court.Kodi kumutengela munthu Ku court ndiye kuti aphwanya malamulo kapena kuwasata?poti malamulo adziko lino chilungamo chimapezeka pa court.

    5. iwe Manda mbuli ndi iweyo coz mwina sunabeledwepo ndi a police, tisapite kutali funsa a mini bus driver mavuto omwe akukumana nawo kuchokela kwa mbava za police za pa nsewu.

    6. Ma minibus driver anabzala okha mchitidwe woipayu ndpo amapacira 4 pampando akudxiwa kuti akapereka kanganyase pa roadblock . Koma tikaonetsetsaso sionse apolice amacita mchitidwe umeneu voz apolice ena ma minibus driver sayesera kupanga za nyasixo. Mwanva kaya a Harry sizowayikira ku mbuyo ma minibus driver nkhani ndlamulo ligwire ntchito bac. Wa police sagwira bus yopanda mlandu ndpo ma passe ter timayenda mwacilungamo

    7. kkkkkkkkkkkkkkkkkk eiiiiiish Titha, Benemac ok guy’s komabe never give up ikathele kwa sing’ano kkkkkkkkkkkkkkkkkk just for jokes

    8. Amene akuona kuti a police ndikalowa zakeeeeee chifirika ndichakuti osamawayetsa dala coz mukamaphwanya malamulo muzikumana nazo basi.ASOVA OPHWANYA MALAMULO ONSE

    9. komabe zina zimangokhala zokambilana pambali not mpakana ku court ayi, and kwinaku kumangokhala kususuka ndi ndalama zacha iniyake.

    10. ndalamayo ikuoneka yambiri panopa,koma nanga zomwe a napangazo anakachita ngozi ndalama imeneyo inakaoneka yochepa kumiyoyo ya athu… ndie aMalawi plz muziganiza kaye musanalakhule zopusa

    11. I think also that its an impossible judgement. If he can afford to raise 100000 to go to driving school then you expect him to pay that fine. I think what is lacking here is accessibility of permission and overtaxing ordinary people. If you tax my minibus more than I make what do you expect ? If they make those laws I think they must look both side so that it balance for business people and government tax. They can’t favour one side and think people will accept. Panja mkazi wanyawani amakala first priority come two years all will be history

    12. Corruption kwambiri pa Malawi coz if I forgot my license, so there’s no means to ask me to pay a lot of money lyk that never umbava basi.

    13. Chilungamo guys

      Amaminibus wa ndachamba.
      Akanyamulanso ma 4-4 akumaonjezeraponso matumba 5 achimanga pamenepo ma 50 kg
      Plus makala
      Madengu ansomba mut
      Achina mbatata ndaziphwao
      Plus mtengo akukhape pati.

      Akutionjeza ma customer fe kwambiri
      Mwachita bwino kwalamula chindaputsa choteroko ena atengerepo phunziro.
      Mbava imasiya kuba ikaona nzake wachotsedwa dzanja kamba kakuba spoon

      Lesson to others

      Good job apolice….

  19. Izo sono nzaboza m’mene ndimaziwila minibus driver ine sangakhale ndi cash yokwana K480 000 nkumalipila mlandu anthuwa ndi mbiya ng’ambe zokwana kkkkk tiyeni muzitisangalasa a 24

  20. Makape apolice amenewa andikwana kwabasi zoima pansewu asiyile a Malawi Roads Authority osati Mbavazi .. Mapazi awoo

    1. ine ndimayendetsa truck 1820 ndiribeso chiphaso koma sanandigwirepo.ndimakafika ku rab process,sunbird ndi jenda daily
      akuwona nkhope eti? kapena poti ndi truck?

Comments are closed.