Kumseu kwavuta: wa minibus wina amulipilitsa K480,000 poyenda opanda chitupa ndi kunyamula ma 4 – 4

203

Chaka chino ndiye zonyengelera kulibe. Apolisi a pamseu akwiya ndipo nonse opitiliza chibwana samalani chifukwa mutha kupeza mavuto.

Mkulu wina oyendetsa minibus wayetsa malodza atagamulidwa kuti alipile ndalama zokwana K480,000 atapezeka kuti amayenda opanda license komanso galimoto yake idalibe zitupa (CoF).

Malinga ndi malipoti, Apolisi adagwila Bambo Julius Pofera mu mzinda wa Lilongwe atawapeza kuti iwo amayendetsa minibus alibe license.

Apolisi ati kuphatikiza apo, adapeza kuti minibus imene amayendetsayo idapezeka kuti inalibe chikalata choiyeneleza kuyenda pamseu (CoF).

Pamwamba pakenso, iwo adanyamula anthu moonjeza. Ati atagwila minibus inali itapakila anthu 20 zomwe ndi zosaloledwa pamseu.

A Pofera atagwidwa anatengeledwa ku bwalo la Milandu mu mzinda omwewo wa Lilongwe kumene anakapezeka olakwa.

Bambo Pofera anapempha bwalo kuti liwachitile chifundo chifukwa kanali koyamba kulakwa komanso ali ndi banja loti alisamale.

Koma Apolisi anapempha bwalo kuti likanthe Bambo Pofera ndi chilango chokhwima kamba koti ngozi zikuchuluka ndipo iwo akufuna anthu atengelepo phunziro.

Poweluza a bwalo anagamula Bambo Pofera kuti alipile K480,000 kapena akagwile wa kalavula gaga kwa miyezi makumi awiri ndi umodzi (21).

Share.
  • Opinion