Tiletsa mitundu ya malonda yokwana 25 kuti adzipanga aMalawi okhaokha – Mumba

Advertisement
Mumba

Vitumbiko Mumba yemwe ndi nduna ya zamalonda wati mwezi uno wa April usanathe akhale akuletsa mitundu ya malonda yomwe akumachita anthu akunja yokwana 25 kuti tsopano adzipanga aMalawi okha okha.

Ndunayi yalankhula izi pa bwalo la Mjamba mu mzinda wa Blantyre pomwe ati cholinga chawo ndi chofuna kuti chuma chikhale m’manja mwa aMalawi.

Iwo atinso katundu monga suga ndi zina zatsika mtengo tsopano chifukwa iwo akuyesetsa kuti aMalawi amve bwino ndipo pompano akhalenso akuyesetsa kuti zitsulo zitsike mtengo.

Ndunayi yati iyo ndi m’modzi mwa anthu amene athamange kuyesetsa kuti a Lazarus Chakwera apitilize kutsogolera dziko lino

“Ine ndili kuno mwawona, ndipo a Chimwendo ndi anzawo ali kudera lina tonse tikuthamangira kuti a Chakwera apambanenso,” anatelo a Mumba

A Mumba atinso zosankhana mitundu sizikuyenera kukhala ndi malo m’dziko la Malawi lino, pomwe ati kulolerana kukuyenera kukhala patsogolo.

Advertisement