Chipasupasu ku Bullets: a Ramadan akuonetsedwa njira yakwawo pamene a Msungama akuthamangila ku Khoti

Nyasa Big Bullets

Mavuto akuona maule sikuti ndi pa galaundi pokha iyayi, ngakhale ku chipinda kumene amayenela kupeza mtendere kuli mavuto osaneneka.

Atayambilanso zosaona pagolo pa masewero awo a sabata latha, timu ya Bullets yaganiza zoimitsa mphunzitsi wa timuyi a Nswazurumo Ramadan.

Nyasa Big Bullets
Zayima ku Bullets

Malinga ndi malipoti, timu ya Bullets yauza a Ramadan kuti apume kaye ndi kulingalila bwinobwino za maphunzitsidwe awo a mpira ku Bullets.

“Sitinawachotse, tingofuna aunikile bwinobwino za tsogolo lawo ndi zomwe akuchita nalo,” atelo a Bullets.

Pa nthawi imene a Ramadan akhale akupemphela kuti Ambuye awakondele kuti asawachotse, timu ya Bullets ikhala ikudalila a Eliya Kananji kuti aitsogolele ku madzi odikha.

Ndipita ku Khoti basi

Ndipo amene anakhalapo wamkulu wa timuyi, Bambo Kondi Msungama aopseza kuti apita ku Khoti kukatenga chiletso.

Iwo ati akukatenga chiletso choti kampani ya Nyasa isapitilize ndi dongosolo lake lofuna kuthandiza Bullets kuziyimila paokha.

“Ndi zofunika kuti Bullets iyime pa yokha, koma dongosolo lake sindikuliona bwino iyayi,” anatelo a Msungama.

Iwo anaonjezelapo kuti auza loya wawo kuti aunike bwino nkhani yofuna kuti Bullets iyambe kuyima payokha ndipo akaona kuti sizikulongosoka apite ku bwalo la Milandu kukamang’ala.

Nkhani yoti Bullets iziyimile payokha yakhala ikumanga nthenje zitadziwika kuti timuyi idatafuna ngati tomato thandizo limene adapatsidwa ndi kampani ya Nyasa manufacturers.

A Nyasa adawapatsa a Bullets theka la biliyoni Kwacha kuti azithandizile kwa zaka zisanu koma patangotha chaka chimodzi, kunapezeka kuti ndalama ija aichecheta ndipo kwangotsala ka chenji kokha.

Advertisement

124 Comments

 1. Team isagulitsidwe iyi, vuto langokhala mbuzi (executive) kulephera kukonza/kugula ma players during off season ndikukonza momwe munali munali mavutomo, kufuna kumangodya dolazo amvekere tisadandaule team ili bwino koopsa lero ndi izi. Very shameful and a disgrace to the pEoPlEz team. Think deeply……!!

 2. Once a bullet, always one!!!. if u argue wth Noma fools, they will bring u down to there level, n beat u wth experience, atayeni ndi ma rubbish awowo, ana opusa akura akulima fodya yemweyo, osatiso kwawo koma ngati ma tenant, tazingokodzerani ma goal, mbatata inu. super league ndiya azibambo.

 3. GUYZ CITIMUCI NDI CATHU BASI, IKANANKHALA KUTI NDI GALIMOTO OLO ITAMACITA MAMBAMPU KOMA SITINGAYITSIKE AI.IKUNGOFUNIKA KUYISALIRA CAKUDYA NDIYIPEPHELELA MOKWANIRA BASI

 4. sungamayo machende ake team yo siyake ndim.mene zinthu zilili ku bullets panopa akuenela anyasa aitenge bas ineyo ndiweni weni sapota wabullets

 5. kondi msungama asayiwale kuti ankatenga katapila kuti ayendetsere team mpaka team kumakhala ndi ngongole zambiri kodi a kondi angapereke more than k100 million kuti neba bullets angwiritsire ntchito pa season? neba bwera ku Lali luban udzawone momwe timayendetsera team with sponsorship or not.

 6. Timu iyi ya Bullets ndi imodzi mwa matimu akulu mmalawi koma ikakhala ndi sponsorship timuyi siyenda bwino kuchuluka anthu adyera,sapota,masapota nawo mmalo moti angopita ku stadium kukachemelela timu akufuna nso malipilo kuchokela ku timu, ngati sapatsidwa mumva komiti iyi sili bho

 7. Amenewa ankapume Kaye kuli bwino mtimu ya BB inkhale yopanda oyiyang’anila zili bwino kwabansi.poti mwana amalila ndi nkodzo wake.

 8. Neba ine sindikubisila kanthu tikuchokela muzinda umodzi!iwe ulindi radio/TV mnyumba mwako zikumakuuza kusuta kuwononga moyo !ndipamene iwe ukupeleka MWANA kuchingambwe zelu ulibe neba

 9. chiphwetherere chatimu,manyaka,manyowa,bibi,nyasi,tunvi,mamima,abwampini,,pitilizani kwnanako,komaso simunati apapa mukulemba practical nde ngat ikukunyerani chonchi nde theory mulimba,,,,mumanyazitsa mpira wakumalawi agalu shupit,, noma kill dem 4 me

  1. ntchito kutukwana basi,,,mpaka kuchita kubalalika ngt akukukakamizani kusuta chamba? mesa mumasuta 2010 inu? oh paja ndiwa expire nchifukwa chake mukupenga shupit

  2. matimu akuluakulu samenya kaye mpira until national team ibwere,matimuwa ndi noma ndisilver basi,,km manyaka onse akhalabe akugwiritsana magobo, ndipo team imene ikuyembekezera relagation (little bullets) ndiye mtsoleri wazogwiritsanagwiritsana magobowa

 10. Guyz tasinthani zinthu kukangana sikungathetse mavuto,,bullets ndi team yayikulu abale ndipo tmakunyadiran kwambiri!!!! Zoluza si nkhan ya chilendo olo real Madrid imaluza kambiranani mwa ntendere guyz!!!!!!!

 11. kkkkkkkkkkkkkk! kampopi,chingambwe,barry,2010,batchala,jaman fc kwinako pitilizan guys,sizatheka ayi,kaya ndi umphawi kaya ndi umbuli,kkkkkkkkkkk! mbola guyz,chi team chomvetsa manyazi kwambiri,kkkkkkkkkkkkkkk!!! dhilu ndi ma blues basi,mkaka wokhaokha

  1. Kkkkkkkkkkk! Big Mbulizi fc,team ya fungo,ya ana maskin opemphetsa,munali ndani inu popanda nyerere? Muziyamika kuti Wanderers sitopa ndikukuthandizani amphawi inu,kkkkkkkk! Kandalama komwe amapeleka anthu opanga chingambwe aja kosakwanira,osamayamika bwa? Ana opusa zedi.

 12. take note every season you so called journelists talks bad about bullets is the season we image championship no wonder this season we are going to be champions i bet

 13. Team imeneyi inatha kalekale chifukwa ndi yakale maseweledwe achikale,ma suporters zopanga zawo zamake zana,kuyambisa ndeu zachikale,satilani nyelele nthawi yafika tsopano yosintha ndi kuiwala za kale

 14. Ineyo ndi wa silver,Kondi is right chifukwa company ikatenga umwini ku bullets ndikudzaona kt sakupanga ma profit monga ankayembekezeka,adzathesa team nkuisiya pa dzuwa..kumbukirani Escom united,komanso kunali Sucoma(Illovo) mmene anathera ma club awa!!

  1. Bullets inakhalapo opanda sponsorship for years I can’ t even remember koma sinathe, achuluka ndi adyera amatenga ngati munda wawo…

 15. Ndikumakhala okhumudwa kwambiri m’mtima mwanga ndikamamva nkhani ngati izi. Chikuvuta ndi chiyani kumvetsetsana Ku team ya fuko BB.Ndikumachita manyazi ine oyikonda bullets (Chris.m. Chiweza. Or Vunja man).

  1. Madala pliz khalani odekha coz mutha kukweza nazo Bp yanu kenako timva kut mwatisya ngati Mfumu ija yaku Thyolo. Zitayeni izi ndi za mpira.

 16. neba kusamva plus makan apapa ndie mmmmmmmm yayang,ana ku ngolo mumva kuti atemanako

 17. Guy koma madziwa kuti kananji ndioosokonexa ali ku wanders technical panel yawwo kunaliso gwedegwede iye uja ama user. Nyanga not talent ine idont see vuto pa ramadhan guy

 18. Ramadan ndiwosanva iye kuyiwala kuti ndi masapota a team yomweyi adamutulusila zikwanje pa ground ndikumuwuza kuti asowe lelo nkumabwelela komweko,kenako anzamva nkhwangwa ili m’mutu

 19. Eeeeee zovuta kuzivesa kwabasi ,, kod pakana season ino ithe tikungokangana????kom ndchan kwenkwen???zina sizinathe zikubwelaso zina ishiiiii my team zandikwanano saname..

 20. Malo mowauza anthu mbola kapena kuti manyi omwe wasankha coach wanu wa flames zimene zukagawa ma poits ku RSA muli buzy kulemba za bulets kkkkkk makape ati cholinga apeze macoment

 21. Makape a Malawi 24 mwasowa cholemba eti kodi team kuimitsa coach ayamba ndi a Bullets? Team iliyonse ili ndi malamulo omwe imatsata polemba coach ndipo gwirizano wa coach ndi team amakhala ma results ndiye ngati team siyikuchita bwino palichifukwa chotsungila coach?

  1. Bale wanga malawi24 siikulakwitsa,ikutiuzammene zilili ku timu ya bb,kwaine ndikamaonera game ya bb vuto sicoach timu ija imasewera bwino,kmano mtima omati anthu amadziwa kale kt ndimachinya akafika kutsogolo amakhala ngati achinya kale kma mpira usanafike paagolo,kusonyeza kt coach ntchito yake waigwira bho bho chikufunika mkungoika mtima akalowa ground ndikudziwa chimene alowera ground,ngati munaonera mpira wamalawi ndi comoros gaba zimene amachita akapeza mpira kutsogolo sizoyenera strikers zimene zija fukwa striker weniweni sangafike goal area mkuseweretsa mpira kt adyetse mpaka goal keeper ayi ndoxhifukwa mpira ukutivuta kumalawi kuno.

Comments are closed.